Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 7

Sewero la Mfumu Edipa [Panja pa nyumba yachifumu ku Thebesi. Khomo lolowera m’nyumbayi Layang’anizana ndi bwalo lomwe payima gulu la anthu. Pambali pa khomoli pali maguwa ansembe. Gulu la anthulo likutsogoleredwa ndi WANSEMBE ndipo onse anyamula nthambi zamitengo. EDIPA akufika kudzera pakhomo la nyumba yachifumu ija.] EDIPA: Inu ana ochokera m’chiwuno mwa Kadima 1 , n’chifukwa chiyani mwayima pamenepa n’kumalira nthambi zofota zili m’manja? Fungo la zofukiza komanso nyimbo zanu zodandawula zangoti bu-u mumzinda- mu. Anthu anga ndisakunamizeni, ine sindikufuna kuti madandawulo anu ndiziwamvera moyenda kuwopera kumva zam’maluwa. N’chifu- kwa chake ndabwera kuti ndidzamve chimvemvemve nkhawa zanu zo- nse. Ndikuganiza kuti nonse mumadziwa kuti ndine mpulumutsi koma- nso mtetezi wanu. Iwe munthu wachikulire, ndiwuze. Iweyo ukuwone- ka kuti ndi amene ukutsogolera anthuwa, choncho yankhula m’malo mwawo. Nena chimene chakuyimitsani mitu kuti mufike mpaka pochi- ta zachilendozi. 1. Kadima: Mbiri imanena kuti Kadima ndi amene anakhazikitsa mzinda wa Thebesi. N’chifukwa chake anthu onse okhala ku Thebesi ankatchedwa ana a Kadima. WANSEMBE: Wolemekezeka mbuyanga mfumu, nokhanso mukutha kuwona anthu amisinkhu yonse asonkhana apawa, omwe akuzunguli- razungulira maguwa ansembewa polirira milungu kuti iwathandize. Ena ndi anyamata amagazi, pomwe ena anawerama kale ndi ukalamba. Ine ndabwera nawo limodzi monga wansembe wawo. Palinso gulu lina lomwe layima patsogolo pa kachisi wa Pala komanso kachisi wa Isimeno yemwe amapereka mawulosi ake pogwiritsa ntchito moto. 2 Ndikabwera ku funso lanu lija, ndikuganiza kuti sindimafunika kuchita kukulakatu- lirani mavuto omwe ali mumzinda muno. Koma popeza mwafunsa, ndi- fotokoza. Mumzinda muno mwagwa matenda osadziwika omwe aku- wononga mbewu zathu kumunda. Matendawa akugwiranso ziweto ndi- po akuchititsa kuti azimayi athu azingopita pachabe. N’kuthekanso mwamva zoti kwabuka mliri wowopsa womwe ukuchititsa kuti anthu azingofa ngati nkhuku zachitopa. Kumanda kwayasama moti sikukuto- pa kububuda matupi a ana a Kadima omwe atsala pang’ono kutheratu psiti. Ndiye popeza ndinu munthu wolemekezeka kwambiri konse kuno, amene amamvana ndi milungu, tati tibwere kudzamang’ala kwa 2