Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 8
Sewero la Mfumu Edipa
inu kuti mutiwuze pamene papindika mchira wanyani. Inuyo muna-
bwera kuno n’kutipulumutsa kwa woyimba wankhanza uja. 3 Sitikayikira
kuti munkadziwa mavuto athu ngakhale kuti panalibe amene anakuwu-
zani. Anthu amakamba mobwerezabwereza za m’mene milungu inaku-
thandizirani kugonjetsa chilombo choyipa ngati chimene chija, chomwe
chinkadya anthu mopanda chisoni. Choncho, mbuyanga mfumu tagwira
mwendo wanu, chonde tithandizeni. Mwina milungu ingakuthandize-
ninso kudziwa chomwe chabweretsa tsokali, kapenanso n’kutheka kuti
munthu wina angakulumeni khutu n’kukuwululirani chinsinsi chomwe
chabweretsa malodzawa, paja amati mutu umodzi susenza denga. Kaya
wina achita kukuthandizani kusenza dengali, kaya ayi, chomwe tikufu-
na ndi chipulumutso basi. Sitikusamalanso za kumene chingachokere.
Chonde chitani zinthu mwanzeru ngati mmene munachitira m’mbuyo
muja kuti chikhulupiriro chathu mwa inu chisayambe kulowa pansi.
Dziwani kuti ngati mutapitirizabe kumangoyang’ana anthu akuvutika
chonchi, zinthu zikhoza kusokonekera. Musayiwale mwambi uja umati,
mfumu ndi anthu. Ngati anthu onse atathera kulichete, simungamala-
mulire mitumbira. Choncho mbuyanga mfumu, konzani kapansi kuti
kam’mwamba katsike.
2. Pala: Pala Athena. Mulunga ameneyu anali ndi akachisi awiri a ku Thebesi. Isimeno: Kachisi wa Apolo komwe anthu
ankakaperekako nsembe zopsereza komwe ansembe ankawona masomphenya okhudza zamtsogolo.
3. Woyimba wankhanza: Akunena za chilombo chamapiko chokhala ngati mkango, chamutu komanso chifuwa cha munthu
wamkazi. Mfumu Layasi itangomwalira chilombochi chinkazunza anthu a ku Thebes. Sichinkawalola kulowa
kapena kutuluka mumzindawu pokhapokha ngati wina atapereka yankho lolondola la ndagi iyi: “N’chiyani
chimayenda ndi miyendo inayi m’mawa, iwiri masana, itatu madzulo?” Anthu amene alephera kupereka yankho
lolondola la ndagiyi ankaphedwa n’kudyedwa ndi chilombochi. Edipa anapereka yankho lolondola (lakuti munthu),
ndipo atachita zimenezi chilombocho chinadzipha ndipo anthu a ku Thebesi anamasuka.
EDIPA: Anthu anga ndisakubisireni, ineyo ndikudziwa bwinobwino
chimene chakubweretsani kuno. Ndikudziwanso kuti mukumva kuwa-
wa. Komabe ngakhale mukumva kuwawa choncho, dziwani kuti palibe
munthu amene akumva kuwawa kwambiri kuposa ine. Aliyense wa inu
akakumana ndi vuto, amavutika yekha mumtima mwake. Koma mavuto
akamachitika chonchi, ineyo monga mfumu yanu ndimamva kupweteka
konse, kwa ineyo komanso kwa nonsenu. Muyenera kuti mukudziwa
zoti nanenso ndakhala ndikusala tulo poyesetsa kupeza njira yothetsera
mavutowa. M’kusinkhasinkha kwanga, ndinapeza njira imodzi yokha.
Ndinawona kuti tikuyenera kumva maganizo a mulungu wathu moti
3