Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 49
Sewero la Mfumu Edipa
n’choti nonse simunabisike kwa ine. Ndikutha kukuzindikirani ngakhale
sindikutha kukuwonani.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Inuyo mwakumana ndi zinthu
zochititsa mantha kwambiri, ndiye n’chifukwa chiyani mwadziwonje-
zeranso mavuto ena podzibowola maso? Ndi mulungu uti amene waku-
limbikitsani kuchita zimenezi?
EDIPA: Ndi Apolo mbale wanga. Apolo ndi amene wandibweretsera
tsoka limeneli. Koma ponena za masowa ndiye sindingamunamizire.
Masowa ndawachotsa ndi manja angawa. Ndikuwona kuti palibenso
chifukwa chokhalira ndi maso ndi moyo wanga womvetsa chisoniwu.
Chilichonsetu chomwe ndingawone sichingandibweretsere chimwe-
mwe?
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Zimene wanenazo ndi zowona
zokhazokha.
EDIPA: Ndi chiyani chimene ndinganene kuti ndingalakelakenso kuchi-
wona? Ndi ndani amene angandipatse moni ine n’kusangalala? Chonde
abale anga, ndichotseni kuno. Ndipirikitseni mumzinda muno. Milungu
yandipatsa chilango chopweteka kwambiri itandiwona kuti ndine wopa-
nda phindu.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Zikuwonekeratu kuti mulibiretu
mtendere wam’maganizo. Ngakhale ineyo ndikanakonda ndikanapanda
kukudziwani, ndipo ndikuganizanso kuti zikanakhala bwino mukana-
panda kubadwa.
EDIPA: Munthu amene anandipulumutsa n’kundimasula miyendo kuti
ndisafe ndi wotemberedwa kwambiri. Chifundo chimene anandichitira
si chabwino ngakhale pang’ono.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Mukunenazo ndi zowona zokha-
zokha. Nanenso ndikanakonda mukanangofa kale lomwelo. Koma na-
nga titani popeza zinachitika kale!
EDIPA: Mwinadi zikanatero sindikanapha bambo anga ndipo anthu
sakanandiwona ndikukwatira mayi anga ondibereka. Tsopano onani
milungu yandinyanyala. Ndingakhalenso bwanji ndi mtendere wam’ma-
44