Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 50
Sewero la Mfumu Edipa
ganizo pamenepo? Ngati pali mavuto owopsa kwambiri amene anthu
amakumana nawo, ndiye ineyo ndawawona ndi kuwagwira komwe.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Koma ine sindikuwona kuti
mwachita zanzeru podzibowola masowo. Kodi simudziwa kuti ndi
bwino kumwalira kusiyana ndi kukhala wosawona?
EDIPA: Usandiwuze kuti zimene ndachitazi si zabwino. Ndipo kungo-
chokera pano sindikufunanso kumva zonena zako. Ukuganiza kuti ndi-
kanakhala kuti ndadzipha ndikanakakumana bwanji ndi bambo koma-
nso mayi anga ku Hade? Anthu awiri amenewa ndinawachitira zonya-
nsa zazikulu kwambiri moti ngakhale nditadzipha sizingakhale zokwa-
nira kufafaniza machimo anga. Mwina ukuganiza kuti kuwona ana anga
kungandipatseko chimwemwe, koma ayi ndithu. Tangowona mmene
anabadwira! Sindingasangalale n’komwe kuwona nkhope zawo. Sindi-
ngasangalalenso kuwona mzindawu limodzi ndi makoma ake. Mtendere
sindingawupeze kuwona zithunzi zopatulika za milungu yathu. Ndine
munthu wotembereredwa kwambiri. Ineyo ndakhala ndikunena kuti
ndidzathamangitsa munthu aliyense amene atapezeke ndi mlandu ume-
newu ndipo ndikanachita zimenezi mopanda chisoni. Ndiye tawonani
matemberero onse aja agwera pamutu panga. Ndine ndani kuti ndize-
mbe chilango chimenechi. Ndine chodetsa chonyansa kwambiri mumzi-
nda muno. Sindikuwona kuti chikanakhala chanzeru kukhalabe ndi
maso n’kumawona nkhope zanu. Ndipo zikanakhala kuti n’zotheka kuti
ndichonse chimene chimandichititsa kuti ndizimva, n’kanachizula ndi
mitsitsi yomwe kuti ndisamvenso zonena za aliyense. Ndikuganiza kuti
munthu angapezeko kamtendere ngati atakhala yekha, osamva kapena
kuwona zimene zikuchitika m’dzikoli. Oo, Thebesi, n’chifukwa chiyani
unandilola kuti ndipezeke kuno? N’chifukwa chiyani sunandiwononge
kapena kundibweza pamene ndinkabwera kwa iwe kuti ndisadzawu-
lulire anthu zokhudza mmene ndinabadwira? Aa, a Polebasi komanso
mzinda wa Korinto, dziko limene anthu ankanena kuti ndiye kwathu.
Munandilera bwino kwambiri moti anthu ankandisirira. Chonsecho
ndinali wodetsedwa kuyambira m’mimba. Tsopano aliyense wadziwa
kuti ndine chinthu chonyansa, munthu yemwe ndi wotembereredwa
kuyambira pakubadwa kwanga. Iwe malo omwe panakumana misewu
45