Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 48
Sewero la Mfumu Edipa
NTHENGA WACHIWIRI: Kayatu! Akungowuza aliyense kuti akufuna
akumane ndi anthu onse kuti awalongosolere zoti ndi iwowo amene
anapha bambo awo komanso kukwatira . . . mwina ndisabwerezenso
mawu amenewa chifukwa ndi owumitsa pakamwa kwambiri. Akuti
akufuna kuti anthu awapirikitse mumzinda muno kuti tsoka limene ali
nalo lisakhudze tonsefe. Koma afowoka kwambiri moti akufunikira mu-
nthu woti aziwachirikiza. Zikuwoneka kuti akumva ululu woposa nsi-
nkhu wawo. Posachedwapa muwawona zipatazi zikangotsegulidwa.
Muwona zinthu zomwe simunayambe mwaziwonapo ndipo sindikuka-
yikira kuti chisoni chikugwirani.
[EDIPA akutuluka m'nyumba yachifumu.]
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Koma chaka chino tiwona malo-
dza ndithu. Munthu womvetsa chisoni iwe, kodi wachita misala kuti
ufike podzipweteka chonchi? Kodi unayambana chiyani ndi milungu
kuti ikuwononge chonchi? Ngakhale kuti pepa sapoletsa chilonda, ndi-
kufuna ndikupepese chifukwa cha mavuto akugwerawa. Kunena zowo-
na wandimvetsa chisoni moti ndangokhala wodzigwira chifukwa ndika-
nakhala wina ndikanagwetsa misozi. Ndili ndi mafunso ambirimbiri
omwe ndikufuna kukufunsa koma pakamwa pangondiwuma!
EDIPA: Ndine munthu womvetsa chisoni kwambiri, munthu wotembe-
reredwa. Zikanakhala bwino ndikanapanda kuliwona dzikoli. Nanga
ndilowera kuti ine?
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Ulowera kudziko lomwe anthu
amathawako, dziko lomwe anthu salifuna.
EDIPA: Mdima wandikuta chifukwa cha munthu wosadziwika yemwe
anabwera pano ndi chowonadi chosatsutsika. Zikungokhala ngati lu-
panga lakuthwa landilasa mumtima. Sindikufunanso kukumbukira kale
langa ngakhale pang’ono.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Koma ndiyetu wakumana nazo
m’bale wanga. Ukungokhala ngati walangidwa kawiri.
EDIPA: Abale anga, zowona mudakasamala za ine? Sindimaganizira
kuti mungapitirizebe kundichitira chifundo ndi kusawona kwangaku.
Pepani kwambiri chifukwa cha machimo angawa. Chikundiwawa
43