Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 47
Sewero la Mfumu Edipa
mwana yemwe anabereka zaka zambiri zapitazo, mwana amene ulosi
unanena kuti adzapha bambo ake n’kukwatira mayi ake. Iye anagona
pakama akulira, pakama yemwe ankagona limodzi ndi Layasi. Kenako
anabereka mwana yemwe anadzakhala mwamuna wake n’kumubereke-
ranso ana. Tikakamba za mmene anafera ndiye sindikudziwa kuti zina-
khala bwanji. Kenako tinangowona a Edipa atulukira. Ife timangowaya-
ng’ana akuyenda molowera uku ndi uku akudziguguda pachifuwa. Pa-
mene amachita zimenezi amatipempha kuti tiwapatse lupanga. Nawo-
nso anali ndi chisoni chachikulu pozindikira kuti anakwatirana ndi mayi
awo. Kenako anangokhala ngati agwidwa ndi chiwanda, moti palibe
munthu amene analimba mtima kuwayandikira. Anakuwa kwambiri
n’kuthamanga kukamenya chitseko chachipinda chomwe Yokasi ana-
dzikhomera ndi phewa lawo moti chokhomera chake chinatotokoka.
Atangolowa anawona Yokasi ali lendelende m’mwamba, atadzimangi-
rira. A Edipa atangowona malodzawo, anayamba kulira mowawidwa
mtima ndipo anachotsa thupi la Yokasi pachingwecho n’kuligoneka pa-
nsi. Zimene zinachitika pambuyo pa zimenezi zinali zoziziritsa thupi.
Tinangowona a Edipa akuthothola kachitsulo kena pachovala cha Yokasi
ndipo anakweza dzanja lawo m’mwamba n’kuzika chitsulocho m’maso
mwawo. Pamene amachita zimenezi amafuwula kowopsa kuti: “Suku-
yenera kudzawonanso zinthu zonse zowopsa zimene wawona, kapena
kudzachitanso zinthu zochititsa mantha zimene wachita! Wawona zi-
nthu zambiri zimene sumayenera kuwona. Choncho kuyambira lero
mpaka m’tsogolo uzingowona mdima wokhawokha.” Amanena mawu
amenewa akubowola maso awowo ndi chitsulocho. Amati akachizika,
magazi amatuluka mowopsa kuchokera m’maso mwawo n’kumayende-
rera mpaka kundevu. Magaziwo samatuluka pang’onopang’ono, ama-
ngokhala ngati mtsinje wodzadza ndi madzi m’nyengo yadzinja. Zimene
achita zatiwopsa kwambiri. Tsoka lochititsa mantha lawomba munthu
ndi mkazi wake ngati mphenzi. Chisangalalo chonse chimene anali na-
cho chasanduka chisoni, moti pano kwatsala n’kulira komanso mavuto
okhawokha. Zikungokhala ngati mavuto onse omwe amagwera anthu
angowakhuthukira nthawi imodzi.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Ndiye iwowo amaganiza kuti
kudzivulazako kuwachepetsera ululu womwe akumva mumtima?
42