Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 46
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Ngati zimenezo zinali zowona, n’chifukwa chiyani munamupe-
reka kwa munthu wachikulireyu m’malo mongomupha?
WANTCHITO: Ankandimvetsa chisoni. Ndiye nditamva zoti mnzanga-
yo amachokera kudziko lina, ndinawona kuti ndingomupatsa kuti aka-
fere kumeneko m’malo moti ndimuphe ndi manja anga. Ndinkawona
kuti sangapulumuke chifukwa anali atavulala kwambiri. Zikuwoneka
kuti mnzangayo anamupulumutsa, koma sankadziwa kuti akusungira
kanjinji, yemwe anali kudzatukusira m’tsogolo. Musangalala kudziwa
kuti mwana amene tikunenayu ndi inuyo. Kubadwa kwanu linali the-
mberero lalikulu.
EDIPA: Kalanga ine, kuteroko ulosi uja unakwaniritsidwa! Oo, kuwala,
ndilole kuti ndikuwone komaliza. Ine ndi munthu wotembereredwa
kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga. Nalonso banja lomwe ndina-
badwira ndi lotembereredwa kwambiri. Chinandiwona n’chiyani kuti
ndiphe munthu yemwe sindinkayenera kumupha?
[EDIPA akulowa m'nyumba yachifumu. Patapita nthawi, NTHENGA WA-
CHIWIRI akutuluka kuchokera m'nyumbayo.]
NTHENGA WACHIWIRI: Pepani kwambiri akuluakulu, zomwe zachi-
tika m’nyumbamu sindizo. Ndikuganiza kuti palibe mtsinje womwe
ungatsuke nyansi komanso zinthu zochititsa nseru zomwe nyumbayi
yakhala ikubisa. Posachedwapa itiwonetsa zosawona. Zimene Yokasi ndi
a Edipa achita m’nyumbamu ndi zowopsa kwambiri.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Bwanjinso? Zowopsatu zomwe
tangomva posachedwapa zatiwiritsa kale mitu. Ukufunanso kutiwuza
chiyani chomwe chingakhale chowopsa kuposa pamenepo.
NTHENGA WACHIWIRI: Mfumukazi Yokasi yadzipha!
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Wati chiyani? Zinakhala bwanji?
NTHENGA WACHIWIRI: Muli ndi mwayi kuti simunawone zimene
zachitika. Zinali zowonekeratu kuti Yokasi amavutika mumtima pamene
amalowa m’nyumbamu. Wayenda chothamanga mpaka kukalowa ku-
chipinda chake. Atangolowa, anakhoma chitseko ndipo anayamba kuli-
rira Mfumu Layasi, yomwe inamwalira kalekale. Iye anakumbukira
41