Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 45
Sewero la Mfumu Edipa
chitike ndikakuwuzani chilungamo.
EDIPA: Akuluakulu, munthuyu ndi wosamva. Mugwireni ntchito!
WANTCHITO: Tayimani kaye! Komatu ndakuyankhani funso limene
munandifunsa! Ndanena kuti ndinedi amene ndinamupatsa mwanayo.
EDIPA: Chabwino, ndiye munamutenga kuti mwanayo? Munamutenga
kunyumba kwanu kapena kwinakwake?
WANTCHITO: Sanali wanga, munthu wina ndi amene anandipatsira.
EDIPA: Munthu wake ndani? Anali wa mumzinda muno kapena ayi?
Nanga dzina lake ndi ndani?
WANTCHITO: Chonde mbuyanga musapitirize kundifunsa mafunso
amenewa! Ndikhululukireni chifukwa sindikwanitsa kuwayankha.
EDIPA: Mukufuna muziyankha mukulira?
WANTCHITO: Ayi, basi ndifotokoza. Mwanayo anabadwira m’nyumba
ya Mfumu Layasi.
EDIPA: Anali mwana wa kapolo wake kapena wa wachibale wake?
WANTCHITO: Ndisanameyi, mafunso amene mukundifunsawa akundi-
sowetsa chonena . . . N’zowumitsa pakamwatu!
EDIPA: Kaya n’zowumitsa pakamwa, ndiwuzeni. Ndikufunika kudziwa
chilungamo.
WANTCHITO: Popeza mwandikakamiza, ndikuwuzani. Anandiwuza
kuti mwanayo anali wake. Ndikuganiza kuti mkazi wanu ndi amene
angakuwuzeni zambiri zokhudza nkhani imeneyi.
EDIPA: Mukutanthawuza kuti iwowo ndi amene anakupatsani mwana-
yo?
WANTCHITO: Inde. Anandiwuza kuti ndikamuphe.
EDIPA: Mayi a mwanayo anali ndani? Yokasi?
WANTCHITO: Inde. Zikuwoneka kuti ankawopa ulosi wina wowopsa
womwe analandira kuchokera kwa Apolo.
EDIPA: Ulosi wake wotani?
WANTCHITO: Ulosi wakuti mwanayo adzapha bambo ake.
40