Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 44
Sewero la Mfumu Edipa
imeneyo ngati mukuyikumbukira kale? Mukufuna kundipala mkamwa?
NTHENGA: Ayi. Ndimangofuna kukuwuzani kuti munthu wayima
apayu, ndi mwana amene unandipatsa uja.
WANTCHITO: Choka apa! Bwanji osaphunzira kukhala chete pa nkhani
zomwe sizikukukhudza?
EDIPA: Bambo, takhalani kaye chete! Musayambe kumunyoza mnza-
nuyu. Zimene inuyo mwanena ndi zimene zili zokayikitsa kwambiri
ndikayerekezera ndi zimene mnzanuyu wanena.
WANTCHITO: N’chifukwa chiyani mwandipsera mtima? Pali chimene
ndakulakwirani?
EDIPA: Sunandiwuze zokhudza mwana amene unamupereka kwa
munthuyu.
WANTCHITO: Zimenezotu ndi zimene munthuyu wakuwuzani! Nanga
ndi ine ngati? Ngati wayiyamba nkhaniyi akufunikanso kuyimalizitsa.
EDIPA: Ngati mutapandatu kutiwuza zowona zenizeni mwamtendere,
dziwani kuti munena zimenezi mukumva ululu wowopsa. Tikukhawu-
litsani.
WANTCHITO: Chonde mbuyanga, musazunze munthu wachikulire!
EDIPA: Asilikali, tamumangani munthuyu asatitayitse nthawi!
WANTCHITO: N’chifukwa chiyani mukuchita zimenezi? Mukufuna
ndikuwuzeni chiyani?
EDIPA: Ndakuwuza kaletu paja. Ndikufuna kudziwa zokhudza mwana
amene munamupereka kwa munthuyu. N’zowona kuti munachitadi
zimenezi?
WANTCHITO: Inde, ndipo ndikanakonda ndikanangofa m’mbuyo
momwemo.
EDIPA: Mwina ndikuwuzeni kuwopsa kwa zimene zingachitike ngati
mutandiwuza zabodza. Ndiwuza asilikaliwa kuti akupaneni, mukapa-
ndabe kuwulula ndiwawuza kuti azikudulani chiwalo chimodzichimo-
dzi mpaka thupi lanulo lithe!
WANTCHITO: Ndikuganiza kuti sizikhala zosiyana ndi zimene zinga-
39