Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 43
Sewero la Mfumu Edipa
Mfumu Layasi?
WANTCHITO: Mwalasa ndithu. Koma sikuti ndinali kapolo, kungoti
ndinakulira m’nyumba mwake.
EDIPA: Nanga unkagwira ntchito yanji?
WANTCHITO: Ndinkagwira ntchito yoweta nkhosa.
EDIPA: Unkaziwetera kuti?
WANTCHITO: Kumapiri a Katero komanso madera ena ozungulira
kumeneko.
EDIPA: Unayamba wakumanapo ndi munthu uyu pamene unkaweta
nkhosa za mbuye wako kumeneko?
WANTCHITO: Munthu wake utiyo?
EDIPA: Uyu wayima apayu. Unayamba wamuwonapo?
WANTCHITO: Aa, sindikumukumbukira.
NTHENGA: Mbuyanga, zimene akunenazi si zodabwitsa chifukwa iye-
yu watheratu ndi ukalamba. Ukalambatu umapha chikumbumtima
n’kuchititsa munthu kufika poyiwala dzina lake. N’kutheka nayenso
anadya mtedza wankhwangwala. Dikirani ndimukumbutse ziwiri zitatu.
Sindikukayikira kuti akukumbukira zonse zomwe zinachitika pa nthawi
yomwe tinakhala limodzi kumapiri komanso madera ena ozungulira.
Iyeyu anali ndi magulu awiri a nkhosa, koma ineyo ndinali ndi gulu li-
modzi. Ndinakhala naye limodzi kwa miyezi isanu ndi umodzi, kucho-
kera m’nyengo yachisanu mpaka m’nyengo yachilimwe. Nyengo yadzi-
nja itafika, ndinatsogolera nkhosa zanga kumakola ndipo nayenso ana-
kusira nkhosa zake kumakola a Mfumu Layasi. Kodi zimene ndikune-
nazi ndi zowona m’bale wanga?
WANTCHITO: Mukunena zowona ndithu. Kungoti ndinayiwala, monga
mukudziwira kuti ndi kale limene lija.
NTHENGA: Usadandawule mnzanga, zimachitika. Ndiyetu ndiwuze
ngati ukukumbukira zimene zinachitika pamene unkandipatsa mwana
wakhanda uja kuti ndizikamulera ngati wanga.
WANTCHITO: N’chifukwa chiyani mukufuna kuti ndikuwuzeni nkhani
38