Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 42
Sewero la Mfumu Edipa
kuti asakulole kudziwa chowonadi chokhudza kumene unachokera.
EDIPA: [Ak uyank hula nd i gulu la anthu.] M’modzi wa inu apite kuka-
tenga m’busa wankhosayo mwamsanga. Musiyeni Yokasi, akuwoneka
kuti amamva kukoma kwambiri kukhala mfumukazi.
YOKASI: Inu ndiye mavuto sadzakuchokani ayi. Ine sindikuletsaninso,
chitani zimene mukufuna. Komanso sindidzakuyankhulitsaninso.
[YOKASI akuchoka chothamanga n'kukalowa m'nyumba yachifumu.]
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: N’chifukwa chiyani mfumukazi
yachoka ndi nkhope yakugwa? Ndikuganiza kuti tikumana ndi mphepo
yamavuto chifukwa cha kukhumudwa kwakeku.
EDIPA: Mphepo imeneyotu iwombe! Musiyeni achite zimene akufuna.
Kaya ndinabadwira banja losawuka chotani, ndikumba mpaka nditape-
za mitsitsi ya kumene ndinachokera. Mwina Yokasi wakwiya chifukwa
akuchita manyazi ndi banja limene ndinabadwira. Zikuwoneka kuti
amafuna amuna ochokera m’mabanja olozeka. Koma ineyo sindinga-
nyozeke chifukwa choti abale anga ndi osawuka. Ndipo ndi wodala
mayi amene anabereka ine. Ndi odalanso azichimwene komanso aziche-
mwali anga. Sindikukayikira kuti angasangalale kwambiri atandiwona
nditakula komanso ndili ndi mphamvu zambiri chonchi. Sindinganyoze
kumene ndinachokera ngakhale kutakhala kochititsa manyazi bwanji!
[Kenako akuponya maso ake chapatali.] Anthuni, ngakhale sindinayambe nda-
wonapo munthu amene tikumudikirayu, ndikuganiza kuti ndi uyo aku-
bwera apoyo. Ngati munayamba mwamuwonapo, sindikukayikira kuti
mungamuzindikire kwambiri kuposa ine.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Inde, munthu ameneyu ndiku-
mudziwa. Anali wantchito wodalirika wa Mfumu Layasi.
[Akufika WANTCHITOYO, ndi wachikulire.]
EDIPA: Iwe nthenga wochokera ku Korinto, ndiyambe ndi kukufunsa
iwe: Kodi munthu umanena uja ndi ameneyu?
NTHENGA: Inde ndi yemweyu ndithu.
EDIPA: Iwe munthu wachikulire. Tandiyang’ana ndipo unene zowona
zokhazokha. Kodi n’zowona kuti m’mbuyomo unali wantchito wa
37