Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 41
Sewero la Mfumu Edipa
NTHENGA: Musafunse ine mlendo, ndikuganiza kuti inuyo ndi amene
mungadziwe kumene ali.
EDIPA: [Ak utem benuk ira k u gulu la anthu.] Kodi pali aliyense pano
amene akudziwa munthu amene akunenedwayu? Munayamba mwa-
muwonapo kwinakwake? Ngati pali amene akudziwa chonde anene.
Zimenezi zingandithandize kudziwa tanthawuzo la mavuto akuchiti-
kawa.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Munthutu akumutchulayo ndi
uja mwatuma kale munthu kuti akamuyitane. Bwanji osawafunsa akazi
anuwo? Iwowatu ndi amene akuyidziwa bwino kwambiri nkhaniyi.
EDIPA: Yokasi, kodi umadziwa zotani zokhudza munthu wapita kuka-
yitanidwa uja? Ndi yemwedi nthengayu akunena?
YOKASI: N’chifukwa chiyani mukungokhalira kundifunsa mafunso?
Ingoyiwalani nkhaniyi. Mukapitiriza mungodzikalasulirapo mavuto!
EDIPA: Zimene wanenazi zikusonyeza kuti munthuyu akunena zowona.
Ndiyitsata nkhaniyi mpaka kumutu. Ndikufunika kudziwa zowona
zenizeni zokhudza kubadwa kwanga.
YOKASI: Chonde musachite zimenezo! Ngati moyo wanu mumawuko-
nda, siyiranitu kuyitosa nkhaniyi. Ingololani kuti ineyo ndivutike, zime-
nezo zikhala zokwanira. Koma mukapitiriza kuwumitsa khosi muputa
mavuto osaneneka.
EDIPA: Osadandawula. Ngakhale zitapezeka kuti makolo anga ndi aka-
polo, iweyo sizikukhudza.
YOKASI: Ndimvereni chonde, ndagwira mwendo wanu! Musachite zi-
menezi.
EDIPA: Komatu ndikuwuze Yokasi, ngakhale utatani ine sindisintha ma-
ganizo. Ndikufuna kudziwa makolo anga enieni.
YOKASI: Komatu ndikunena izi pofuna kukutetezani.
EDIPA: Zimene ukundiwuzazi zikungochititsanso kuti mutu wanga
uwire kwambiri.
YOKASI: Oo, munthu wotembereredwa iwe! Ndikupempha mulungu
36