Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 40
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Kuteroko munali m’busa waganyu?
NTHENGA: Inde, komatu ngakhale zili choncho ndi ineyo amene ndina-
kupulumutsani.
EDIPA: Ndiye mutanditola, ndinkawoneka bwanji? Ndinali bwinobwi-
no?
NTHENGA: Yang’anani akakolo anuwo muwone mmene
munkawonekera.
EDIPA: Aa, n’chifukwa chiyani mwatchula tsoka langa lakalekale?
NTHENGA: Ndinakupezani akakolo anuwo atabowoledwa ndi chitsulo
komanso atakumangani miyendo. Ndi ineyo amene ndinakumasulani.
EDIPA: Zipsera zimenezi zimandiwawa kwabasi. Ndakhala ndi zipsera
zimenezi kungochokera ndili mwana.
NTHENGA: N'chifukwa chaketu anakupatsani dzina muli naloli. 5
5. Dzina lakuti Edipa limatanthawuza "wotuma pamazi."
EDIPA: Komano tandiwuzeni, n’chifukwa chiyani makolo anga anandi-
chita zimenezi?
NTHENGA: Sindikudziwa. Munthu amene anakuperekani kwa ineyo
ndi amene anganene zambiri.
EDIPA: Mukutanthawuza kuti pali munthu winanso amene anakupatsa-
ni mwanayo? Moti simunamutole patchire?
NTHENGA: Inde, sindinamutole patchire. M’busa wina ndi amene
anandipatsa mwanayo.
EDIPA: Mungamukumbukire mutamuwona? Ankaweta nkhosa za nda-
ni?
NTHENGA: Anthu amati ankaweta nkhosa za Mfumu Layasi.
EDIPA: Mukutanthawuza mfumu yomwe inkalamulira kuno zaka za-
mbiri zapitazo?
NTHENGA: Inde. Zikuwoneka kuti anali wantchito wa Mfumu Layasi.
EDIPA: Adakali ndi moyo m’busayo? Ngati ndi choncho, mumadziwa
kumene amakhala?
35