Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 39
Sewero la Mfumu Edipa
kuti ulosi wa Apolo ukwaniritsidwe pa ine.
NTHENGA: Kuteroko kuthawathawa konseku munkawopa kukwatira
mayi anu komanso kupha bambo anu?
EDIPA: Ndi momwemo ndithu, moti sindigona tulo ndi nkhani imeneyi.
NTHENGA: Koma mukudziwa kuti mantha amenewa mumangowona
kukhala nawo?
EDIPA: Mukutanthawuza chiyani? Mesa makolo anga ndi . . .
NTHENGA: Chifukwa chake ndi choti palibe ubale uliwonse pakati pa
inuyo ndi a Polebasi.
EDIPA: Koma ndiye mwandipindatu pamenepo! A Polebasi si bambo
anga?
NTHENGA: Iwowo n’chimodzimodzi ineyo. Monga mmene zilili kuti
ineyo si bambo anu, ndi mmene zilili ndi a Polebasi.
EDIPA: Bwanji mukudziyerekezera ndi bambo anga?
NTHENGA: Nkhani ndi yakuti, a Polebasi alowa m’mandawa si bambo
anu ngati mmene zilili kuti ineyo si bambo anu.
EDIPA: Nanga n’chifukwa chiyani ankanena kuti ndine mwana wawo?
NTHENGA: Ngati mukufuna kudziwa ndikhoza kukuwuzani. Ineyo ndi
amene ndinakuperekani ngati mphatso kwa iwowaja kuti azikulelani.
EDIPA: Komatu ankandikonda kwambiri. Zikanatheka bwanji kuti azi-
ndikonda choncho ngati sindinali mwana wawo weniweni?
NTHENGA: Chifukwa chake ndi choti ndisanakuperekeni kwa iwowo,
akazi awo aja anali owuma. Anakhala zaka zambirimbiri wopanda
mwana. N’chifukwa chake ankangokuwonani ngati mwana wawo
weniweni.
EDIPA: Mwafotokoza kuti munandipereka kwa a Polebasi ngati mpha-
tso, koma nanga inuyo munanditenga kuti? Munangonditola penapake?
NTHENGA: Ndinakutengani kumapiri.
EDIPA: Munkakataniko kumapiriko?
NTHENGA: Ndinkaweta nkhosa za mbuye wanga.
34