Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 38
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Dzina lawo ndi a Merope, akazi a bambo anga a Polebasi.
NTHENGA: N’chifukwa chiyani mumachita nawo mantha mayi anuwo?
EDIPA: Bambo, ineyo ndinawuzidwa ulosi winawake wochititsa mantha
kwambiri.
NTHENGA: Ndi nkhani yachinsinsi kapena mukhoza kundibenthulira-
ko?
EDIPA: Ayi, ndikhoza kukunyotsoleraniko pang’ono. Apolo anandiwu-
za kuti ndidzapha bambo anga n’kukwatira mayi anga. Chimenechi
n’chifukwa chake zaka zambiri zapitazo ndinathawa kwathu ku Korinto.
Nditabwera kuno, zinthu zinayamba kundiyendera bwino monga mme-
ne mukuwoneramu.
NTHENGA: Ndiye mukutanthawuza kuti munathawa ku Korinto
chifukwa chowopa kukwatira mayi anu?
EDIPA: Inde, komanso ndinkawopa kuti ndikhoza kudzapha bambo
anga.
NTHENGA: Mbuyanga, popeza ndabwera kudzakuwuzani uthenga
wosangalatsa, bwanji ndikumasuleninso kunsinga za mantha amenewo?
EDIPA: Inde, ungachite bwino kwambiri. Ndiwuze chonde ulandira
chiwongoladzanja.
NTHENGA: Musandandawule ndi zachiwongoladzanjazo, ineyo nda-
bwera kudzakutengani kuti mubwerere kwanu ku Korinto. Anthu aku-
kuyembekezerani kuti mukakhale mfumu yawo.
EDIPA: Ayi. Sindikufuna kubwerera kwathu mayi anga akadali moyo.
NTHENGA: Mwana wanga, zikuwonekatu kuti sukudziwa chimene
ukuchita . . .
EDIPA: [Ak um ud ula maw u nthengayo .] Mukutanthawuza chiyani? Ta-
ndiwuzeni bwinobwino musamangondisiya m’malere!
NTHENGA: . . . ngati mukukhala moyo wothawathawa n’kumawopa
kubwerera kwanu pachifukwa chimenecho, ndikufuna ndikuwuzeni
kuti mukungotaya nthawi yanu komanso mukungodzivuta.
EDIPA: Ayi sindikudzivuta. Ndikuchita zimenezi chifukwa sindifuna
33