Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 37
Sewero la Mfumu Edipa
Nanga ine ndagwira lupanga n’kuwapha ngati? Kapenatu mwina afa
chifukwa choti anandipukwa? Ayi ndithu. Sindidzakhulupiriranso ma-
wulosi ochokera kwa owombeza mawula kapena kwa aneneri omwe
akasowa zochita amayamba kuwuza anthu mabodza. Imfa ya bambo
anga yanditsimikizira kuti anthu amenewa ndi atambwali otheratu.
YOKASI: Inetu ndinakuwuzani.
EDIPA: Indedi unanena, koma kungoti mantha ndi amene anandiphi-
mba m’maso.
YOKASI: Ndiyetu lekani kuda nkhawa ndi mawulosi osachitikawa.
EDIPA: Koma chimene ndikuwopa tsopano ndi mayi anga. Mayi anga
adakali ndi moyo. Ndikanakonda nawonso akanamwalira mwachangu.
YOKASI: Kodi munthu amene akukhala ndi moyo n’kumasankha yekha
zochita, angamachitenso bwanji mantha ndi mawulosi osachitika. Akho-
zatu kumangokonza mapulani ake n’kumayesetsa kuti zimene akufuna-
zo zitheke. Angaderenso nkhawa ndi chiyani? Si nanga tsogolo lake lili
m’manja mwake? Ingogwiritsani ntchito moyo wanuwu mwaphindu,
chitani zonse zomwe mungathe kuti zinthu zikuyendereni. Osada nkha-
wa ndi zan’kutuzi. Munthu amene anakuwuzani kuti mudzakwatira
mayi anuyo adzakwatira ambuyake! N’zowona kuti m’maloto anthu
ambirimbiri anakwatirapo mayi awo, koma anthuwo anangoziponyera
kunkhongo n’kumapitiriza kuchita zinthu zotukula miyoyo yawo ndipo
mpaka pano zinthu zikuwayendera bwino.
EDIPA: Zonse zimene ukunenazo zikanakhala zomveka zikanakhala
kuti mayi anga anamwalira. Koma popeza akadapuma, mantha sanga-
ndichokeretu chifukwa chilichonse chikhoza kuchitika.
YOKASI: Komabe, imfa ya bambo anuyi yatikhazika mitima pansi. Yati-
thonthoza kwabasi.
EDIPA: Indedi, nkhani imeneyi ndi yosangalatsa kwambiri. Atsala ndi
mayi anga okhawo basi. Akangomwaliranso amenewa mpamene ndita-
yambe kugona tulo tabwino chifukwa sipakhalanso munthu wondiyika
pachiwopsezo.
NTHENGA: Kodi dzina la mayi anu mukunenawo ndi ndani?
32