Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 36
Sewero la Mfumu Edipa
NTHENGA: Ndi momwemo ndithu, simunaphonye. Mukapeza kuti
ndikunama mundisende chikopa changachi ngati mbuzi.
YOKASI: [Ak uyank hula nd i k ap o lo wak e.] Iwe, tafulumira ukayitane
mbuye wako m’nyumbamu!
[KAPOLOYO akulowa m'nyumba yachifumu. Posakhalitsa EDIPA akutulu-
kira.]
EDIPA: Yokasi mkazi wanga wokondedwa, n’chifukwa chiyani wandi-
yitananso kuti ndibwere panja pano?
YOKASI: Bwerani mudzamve zimene munthuyu akunena. Mukamva
zimene atakuwuzeni, muwona kuti mawulosi amene milungu imanena
ndi opanda ntchito mpang’ono pomwe.
EDIPA: Munthuyu wachokera kuti?
YOKASI: Wachokera ku Korinto ndipo wabweretsa uthenga wonena za
a Polebasi, bambo anu. Akuti abzala chinangwa.
EDIPA: Wati bwanji? Bambo, ndikufuna kumva uthengawu kuchokera
pakamwa panu. Ndiwuzeni uthenga wonse umene mwabweretsa.
NTHENGA: Ndikukuwuzani a Edipa muli apa, a Polebasi bambo anu,
amwalira. Bambo anu aja kulibenso.
EDIPA: Achita kuphedwa kapena amwalira ndi matenda enaake?
NTHENGA: Amwalira ndi ukalamba, monga mukudziwira mmene
moyo wathuwu umathera munthu akakhala masiku ambiri padzikoli.
Thupi lawo linafika potha ntchito.
EDIPA: Ukutanthawuza kuti sanamwalire ndi matenda enaake?
NTHENGA: Inde, thupi lawo linangofika potopa moti atsamira mkono
chifukwa cha ukalamba.
EDIPA: Mkazi wanga umanena zowona! Mawulosidi ndi osathandiza
ngakhale pang’ono. Aneneri am’mutu omwe amatumikira kukachisi wa
Apolo komanso ena onse, omwe amalandira mawuthenga kuchokera
kwa mbalame akuyenera kuwonongedwa. Ndi anthu angati omwewa
omwe anandinamiza kuti ndidzapha bambo anga. Nanga tawonani,
bambo anga amwalira ndi ukalamba ndipo akwiriridwa kale m’nthaka.
31