Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 35

Sewero la Mfumu Edipa kuti mutichotsere mavuto atigwerawa. Pakuti tsopano tili ndi mantha aakulu. Mantha athu ndi aakulu mofanana ndi mmene zimakhalira anthu akawona amalinyero oyendetsa chombo chimene akwera akulira pothedwa nzeru ndi namondwe wowopsa. [YOKASI akuyika nsembe zake paguwa. NTHENGA akulowa. Nthengayu ndi munthu wachikulire.] NTHENGA: Wawatu wawa, kodi mungandilozere kunyumba kwa amfumu? Ndabwera ndi uthenga woti ndiwapatsire. TSOGOLERI WA GULU LA ANTHU: Nyumba yawo ndi imeneyi ndipo mwachita mwayi kuti mwawapeza ali pakhomo. Akupereka nsembe apowo ndiye akazi awo. NTHENGA: Mulungu akudalitseni mfumukazi yanga ndipo banja lanu likhale pamtendere mpaka kalekale. YOKASI: Nanunso mulungu akudalitseni. Mawu anu akusonyeza kuti ndinu munthu wabwino kwambiri. Ndiye tikuthandizeni bwanji? N’chi- yani chakubweretsani kuno? NTHENGA: Mfumukazi yanga, ndabwera ndi uthenga wabwino wopita kwa mwamuna wanu. YOKASI: Mwachokera kuti? NTHENGA: Ndachokera ku Korinto. Ndiye mosachulukitsa gaga, ndi- kuwuzeni uthenga umene ndadza nawo. Sindikukayikira kuti musanga- lala nawo kwambiri, ngakhalenso kuti mwina mukhoza kukhumudwa nawo. YOKASI: Zingatheke bwanji kuti uthenga umodzi ukhale wosangalatsa komanso wokhumudwitsa? NTHENGA: Anthu a ku Korinto akufuna kuti a Edipa akakhale mfumu yawo kumeneko, moti andituma kuti ndidzawatenge. YOKASI: Mukutanthawuza chiyani? Mukufuna kundiwuza kuti Mfumu Polebasi yamwalira? NTHENGA: Inde, yamwalira ndipo yayikidwa kale m’manda. YOKASI: Mwati bwanji? Bambo a mwamuna wanga amwalira? 30