Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 34
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Ngati zimene anganene zikufanana ndendende ndi zimene
wafotokozazi, ndiye kuti mavuto alipo.
YOKASI: N’chiyani chomwe chili chapadera pa zimene ndakuwuzanizi?
EDIPA: Si paja wandiwuza kuti munthuyo ananena kuti Layasi anaphe-
dwa ndi gulu la achifwamba. Ngati atanena zofanana ndi zimenezi ndi-
ye kuti si ine amene ndinapha Layasi, chifukwa palibe munthu amene
angalephere kusiyanitsa munthu m’modzi ndi gulu la anthu. Koma aka-
ngonena kuti anaphedwa ndi munthu m’modzi, ndiye kuti mlandu
umenewo ugwera pamutu panga.
YOKASI: Komatu zimenezo ndi zimene anandiwuza. Ndipo ndikuga-
niza kuti sangasinthe poyerayera. Mzinda wonse unamumva akunena
zimenezi. Koma ngakhale atasintha zonena, sizingasinthe chilichonse
n’kuchititsa kuti ulosi umene Layasi anawuzidwa ukwaniritsidwe. Chi-
fukwatu Apolo ananena kuti Layasi adzaphedwa ndi mwana yemwe
adzabereke ndi ine. Nanga mwana watsokayo ali kuti? Si anafa kalekale?
Kwa ineyo sindikufunikanso umboni wina wonditsimikizira kuti ulosi-
wu unalephereka mochititsa manyazi.
EDIPA: Zimene ukunenazo ndi zowona. Komabe ndingakonde kuwona-
na ndi wantchitoyo basi.
YOKASI: Musadandawule mbuyanga, abwera. Koma panopa tiyeni kaye
mukalowe m’nyumba.
[EDIPA ndi YOKASI akulowa m'nyumba yachifumu. Kenako YOKASI akutu-
luka limodzi ndi akapolo ake awiri n’kupita pamene pali guwa lansembe la Apolo
lomwe lili pafupi ndi khomo lolowera m’nyumbayo.]
YOKASI: Inu akuluakulu a Thebesi, ndawona kuti ndi bwino ndidzape-
mbedze milungu yathu pamaguwa opatulikawa. Ndachita zimenezi
chifukwa a Edipa ali ndi nkhawa yayikulu komanso asokonezeka maga-
nizo. Iwo akungoganizira zimene zinachitika kalekale m’malo mopeza
njira yothetsera mavuto akungowunjikanawa. Zikuwoneka kuti sakuga-
nizanso bwinobwino. Akungomvetsera munthu aliyense amene akuwa-
fotokozera uthenga wochititsa mantha, moti asiya kumvetsera zonena
zanga. [Ak uyam ba k up em p hera.] Apolo, tabwera kudzalira pamaso pa-
nu. Tabwera kwa inu ndi nsembe komanso zofukizira ndipo tikupempha
29