Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 33

Sewero la Mfumu Edipa wafotokoza aja. Munthu yemwe ankayendetsa galetalo anayamba ku- ndithupsa n’kumanena kuti ndipatuke pansewu. Koma ine sindinkafuna moti tinayamba kukanganapo. Zimenezi zinachititsa kuti munthu wa- chikulire uja alowererepo. Kunena zowona ndinakwiya kowopsa, moti ndinawumbudza munthu ankayendetsa galetayo n’kumugwetsera pa- nsi. Koma pamene ndinkadutsa pafupi ndi galetalo, munthu wachikuli- reyo anandikong’ontha pamutu ndi ndodo yake mawulendo awiri. Pa- menepo mkwiyo wanga unayaka kwambiri moti nanenso ndinamuku- ntha ndi ndodo yomwe inali m’dzanja langa ndipo anagwera munsewu n’kumwalira. Ena aja anayamba kulimbana nane moti ndinapengeratu ndi nkwiyo n’kuphanso otsalawo. Ngati munthu ameneyo anali Layasi ndiye kuti ndine munthu wotembereredwa kwambiri. Ndikuganiza kuti milungu imadana nane. Ngati zimene ndikuganizazi zilidi zo- wona, ndiye kuti sindikuyenera kulandiridwa ndi munthu aliyense pa- khomo pake komanso munthu aliyense sakuyenera kuyankhula nane. M’malomwake, anthu ayenera kundithamangitsa m’nyumba zawo. Ndi manja angawa ndinapha munthu n’kudzayipitsanso pogona pake. Kodi sitinganene kuti munthu wotero ndi woyipa kwambiri? Ineyo ndikuye- nera kuthamangitsidwa kuno ndipo sindikufunikanso kukaponda nthaka ya kwathu ku Korinto kapena kukakumana ndi achibale anga. Ngati nditangoyerekeza kuchita zimenezi, ulosi wa Apolo ukhoza ku- kwaniritsidwa. Ndikhoza kupezeka kuti ndakwatira mayi anga n’kupha bambo anga ondibereka a Polebasi. Choncho ngati mukunena kuti zi- mene ndikumvazi ndi zochokera kwa mulungu, apo ndiye mantha andigwira kwambiri. Mwinatu Apolo akufuna kundithamangitsa kuno kuti ndibwerere kwathu n’kukakwaniritsa ulosi wake uja. Koma ayi ndithu, sindilola kuyenda m’njira imeneyi. Kuli bwino ndife kusiyana n’kuchita chonyansa ngati chimenechi. MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Mbuyanga mfumu, zimene mwanenazi nafenso zayamba kutiwopsa. Koma musataye mtima kufi- kira wantchito wapita kukayitanidwayo atabwera. EDIPA: Ndidikira moleza mtima mpaka munthu ameneyo abwere. Si bwino kumataya mtima msanga. Nguluwe inalira msampha utaning’a. YOKASI: Ndiyeno akabwera mukuyembekezera kuti mumva zotani? 28