Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 54
Sewero la Mfumu Edipa
nda makolo.
[Akuyankhula ndi gulu la anthu.] Anthu a ku Thebesi, awa akhala ana anu
tsopano. Musalole kuti akule movutika. Musayiwale kuti mwana wa
mnzako ndi wako yemwe, ukachenjera manja umadya naye. Chonde
asamalireni asadzafe mbeta. Nawonso ndi abale anu, musalole kuti
adzamve zowawa zangati ndakumana nazo inezi. Ndagwira mwendo
wanu, chonde amvereni chisoni. Tawonani misinkhu yawoyi, adakali
anthete ndipo akumana kale ndi mavuto oposa misinkhu yawo. Ndilo-
njezeni kuti muziwathandiza. Ndiponso inu ana anga, pali zinthu
zambiri zimene ndikanakonda nditakuwuzani, koma sinditero pakuti
ndinu ana. Koma ndikukupemphani kuti muyesetse kuti musadzakhale
ndi moyo wovuta ngati wangawu.
KIREYO: Basi mwalira mokwanira, pitani mukalowe m’nyumba.
EDIPA: Ndikumvera ngakhale kuti si zimene ndimafuna.
KIREYO: M’kupita kwa nthawi, zinthu ziyambiranso kuyenda bwino.
Osadandawula.
EDIPA: Ndipitadi, koma choyamba ndikufuna ulumbire kaye.
KIREYO: Mukufuna ndilumbire chiyani?
EDIPA: Lumbira kuti undichotsa kuno, sindikufunanso kukhala ku
Thebesi kuno.
KIREYO: Ndi mulungu yekha amene angakuchitireni zomwe mukufu-
nazo.
EDIPA: Ukutanthawuza kuti wavomera?
KIREYO: Musandiyike mawu mkamwa. Ine sindikufuna kumayankha
ndisanaganize. Ndimawopa kudzilowetsa m’mavuto.
EDIPA: Ndiyetu nditulutse mumzinda muno kuti usalowe m’mavuto-
wo.
KIREYO: Chabwino, koma musatenge anawa.
EDIPA: Ayi, sindilola zimenezo. Ukuganiza kuti ukandilanda anawa
ndiye nditsala n’chiyani?
KIREYO: Musayiwaletu kuti mulibenso mphamvu zomangolamula
49