Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 55
Sewero la Mfumu Edipa
chimene mukufuna. Sinunso mfumu ayi, ndinu munthu wamba.
[KIREYO, EDIPA, ANTIGONE, ISIMENE ndi ANTCHITO aja akulowa
m'nyumba yachifumu ndipo sewero likuthera pomwepo.] 7
7. Sewereoli limatha zisakudziwika bwinobwino kuti Edipa anachokadi ku Thebesi kapena ayi. Malinga ndi nthano
zina zakale kwambiri zomwe Sophocles anagwiritsa ntchito polemba seweroli, Edipa anakhalabe ku Thebesi kwa
kanthawi mzika komanso Kireyo asanamuthamangitse mumzindawo. Komanso zimene Kireyo ananena
chakumapetoku, zikusonyeza kuti anakonza zoti adikire mpaka atamva kuchokera kwa Apolo zenizeni zoti achite
ndi Edipa. Komabe zimawoneka kuti m'buku lina lotchedwa Illiad, Homber analemba kuti Edipa anafera ku Thebesi
ndipo pamaliro ake anthu a ku Thebesi anachita miyambo komanso masewera osiyanasiyana pomulembekeza.
50