Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 53
Sewero la Mfumu Edipa
uwasamalire bwino mpaka atakula. Koma choyamba alole kuti abwere
adzagwire manja angawa ndisananyamuke kuti ndilire nawo limodzi.
Kireyo m’bale wanga, iwe munthu wamtima wabwino, ngati nditawa-
gwira ndi manja angawa, kulikonse kumene ndingapite ndiziwakumbu-
kira. [ANTCHITO ena ak ufik a nd i ANTIGONE k o m anso ISIMENE k u-
chokera m'nyumba yachifumu.] Ndikumva kuti kukubwera anthu, kodi ndi ana
anga okondedwa amene akulirawo . . . ? Kodi Kireyo wandichitiradi
chifundo ponditumizira ana anga, ana omwe ndimawakonda kwambiri?
Kodi ndi zimenedi zikuchitika?
6. Ana aamuna awiri a Edipa ndi Utiko komanso Polenike ndipo ayenera kuti pa nthawiyi anali ndi zaka khumi
mphambu zisanu kapena zaka khumbi mphambu zisanu ndi chimodzi ndipo sanali aakulu moti n'kukhala
pampando wa bambo awo monga mfumu.
KIREYO: Inde. Ndawabweretsa kwa iwe kuti uwakumbatire. Ndiku-
dziwa kuti ana amenewa umawakonda kwambiri ndipo mwina mtima
wako ungapepukeko.
EDIPA: Ndimakukondani ana anga moti ndikukufunirani zabwino zo-
nse. Ndikupempha kuti mulungu akuyang’anireni komanso akuchitireni
zabwino osati zangati zimene zachitikira inezi. Ana anga, kodi muli ku-
ti? Bwerani kuno, bwerani ndikukumbatireni. Inuyo ndinu azichemwali
anga tsopano. Gwirani manja omwe achotsa maso angawa n’kuwachi-
titsa kuti aziwoneka mdima wandiweyani. Tawonani pomwe panali
maso anga pangotsala zigompholera zokha. Ineyo ndinali bambo yemwe
ngakhale ndinali ndi maso sindinkapenya, moti mosadziwa ndinabereka
inu ndi mayi omwe anandiwonetsa dzikoli. Pepani kwambiri ana anga.
Ngakhale kuti pano sindikuthanso kuwona, sindingakuyiwaleni nga-
khale pang’ono. Ana anga muvutika chifukwa cha ine moti mwina
anthu ena azikusalani, sazikuyitanani m’mapwando awo. Mukafika
msinkhu wokwatiwa, ndikuda nkhawa kuti mwina sipadzapezeka mu-
nthu woti akukwatireni chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zomwe
bambo wanune ndinachita. Pepani kuti munachita tsoka kukhala ndi
bambo wotembereredwa ngati ine. Bambo anu anapha bambo awo, ndi-
po kenako anakwatira mayi awo ndipo anabereka inuyo. Anthu aziku-
nyozani kwambiri chifukwa cha zimenezi. Ndiye ndi ndani angalimbe
mtima kuti akukwatireni? Palibe ana anga. Inuyo mudzakula mpaka
kuchita chisira ndipo mudzafa muli mbeta. Ana atsoka inu, mukula opa-
48