Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 52
Sewero la Mfumu Edipa
kundichitira chifundo, ndichotse ku Thebesi kuno. Ndithamangitsire
kumalo omwe sikukhala munthu aliyense komanso kumene sikungafike
munthu.
KIREYO: Zimenezo ndichita ndithu, koma choyamba ndikufuna ndimve
kaye maganizo a mulungu wathu.
EDIPA: Komatu paja Apolo ananena kale zomwe tikuyenera kuchitira
munthu amene wabweretsa tsokali. Anati munthu ameneyo akuyenera
kuwonongedwa. Tsopanotu zadziwika kuti munthu ameneyo ndi ineyo,
ndiye n’chifukwa chiyani ukuzengereza?
KIREYO: Sindikuzengereza, ndichita momwemo ndithu. Komabe ndi
zimene zachitikazi, tingachite bwino kudziwa zenizedi zimene akufuna
kuti tichite.
EDIPA: Kodi ukufuna uzikamupempha kuti ndikhalebe ndi moyo mme-
ne ndililimu?
KIREYO: Zimenezo ndiye zoyenera kuchita. Ndipo nanunso mukufuni-
ka kuyamba kukhulupirira kwambiri milungu.
EDIPA: Inde, ndikuyeneradi kutero. Ndiye ndili ndi ntchito yoti uchite
usanakapemphe zimenezi. Mayi uyo ali m’nyumbayo, chonde umuko-
nzere mwambo wamaliro. Iweyo ndi amene uli ndi udindo wochita mi-
yambo yonse yamaliro popeza ndi mchemwali wako. Koma usayerekeze
kuchititsa kuti mzinda wa bambo anga ukhale wodetsedwa chifukwa
choti ine ndikupitirizabe kukhala kuno. Ndilole kuti ndizipita kuti ndi
kakhale kumapiri a Katero, komwe ndinakatayidwa. Pamene bambo
anga ndi mayi anga anali moyo, anasankha kuti manda anga akakhale
kumeneko. Choncho ndikufuna kukafera kumeneko potsatira zomwe
makolo anga ankafuna. Koma chimene ndikudziwa n’choti sindifa ndi
matenda kapena mavuto ena aliwonse. Ndikudziwa kuti sindingadzafe
popanda chinachake chowopsa kundichitikira. Koma kaya ndidzafa
bwanji, ndisiyeni ndichoke kuno. Ponena za ana anga aamuna awiri,
sindikusenzetsa udindo woti uziwasamalira, chifukwa akula tsopano.
Ndikudziwa kuti akhoza kudzisamalira pawokha tsopano. 6 Koma pone-
na za ana anga aakazi awiri omwe sanazolowere kukhala popanda ine,
omwe ankadya chakudya chomwe ndinkadya, ndikukupempha kuti
47