Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 51
Sewero la Mfumu Edipa
itatu, iwe amene unayamwa magazi a bambo anga omwe ndinawakhetsa
ndi manja anga, kodi ukundikumbukirabe? Kodi ukukumbukira zimene
ndinachita pamaso pako komanso zomwe ndinachita nditabwera kuno
ku Thebesi? Aa, ndi kotembereredwa kubadwa kwanga! Tawonani mi-
mba imene ndinachokera inaberekanso ana ena. Ana a ine munthu ye-
mwe ndinachokera m’mimba yomweyo. Tawonani ndinapanga banja
lobweretsa chitonzo la anthu apachibale. Tandiwuzani anthuni, palinso
chonyansa china chomwe chingapose pamenepa? Chonde ndichotseni
kuno mwansanga, kandibiseni kudziko lina kunja kwa mzinda wa
Thebesi. Mukhozanso kungondipha, kapena kundimangirira chimwala
champhero m’khosi n’kukandiponya m’nyanja kuti ndisadzawonekenso
mpaka kalekale. Bwerani, mugwire thupi la munthu wotembereredwa.
Musachite nane mantha popeza nthenda yomwe ndikudwala ndi yoti
singagwirenso munthu wina.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Kireyo akubwera. Ndikuwona
kuti wabwera pa nthawi yake kuti achite zimene a Edipa akutipemphazi.
Popeza akuchoka, Kireyo ndi amene watsala amene angateteze mzinda
wathuwu.
EDIPA: Kalanga ine, ndikwanitsa bwanji kuyankhula naye? Ndimuwuza
chiyani kuti andikhululukire? Si kale pamene ndinamuchititsa kumva
zowawa.
[Akufika KIREYO.]
KIREYO: A Edipa, ndabwera kuti ndidzakuyimbeni mlandu pa zimene
munandichitira. Koma choyamba, ngati moyo wayamba kukunyansani,
chonde lemekezani mulungu wathu dzuwa, yemwe amachititsa kuti
zinthu zimere ndipo musawonetse anthuwa chonyansa chotere. Chifu-
kwatu ngakhale dziko kapena kuwala kapena mvula yopatulika singa-
kondwere ndi zimene mwachitazi. [KIREYO ak uyam ba k uyank hula nd i
antchito.] Tawatengani awa mulowe nawo m’nyumbamu mofulumira. Chinthu
chabwino kwambiri chimene tingawachitire ndi kuwalola kuti awonane
ndi ana awo kuti awawuze mawu omaliza.
EDIPA: Kireyo ndiwe munthu wabwino kwambiri. Sindimaganiza kuti
ungandichitire zinthu mwachifundo chonchi. Koma ngatidi ukufuna
46