Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 31
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Panopa sindilinso moti n’kumayankha mafunso a munthu. Ta-
ndiwuze, kodi Layasi anali wowoneka bwanji? Nanga anali ndi zaka
zingati pamene ankaphedwa?
YOKASI: Anali wamtali komanso wachikulire, moti imvi zinali zitaya-
mba kumutu kwake. Mawonekedwe ake sanali osiyana kwenikweni ndi
mmene mumawonekera inumu.
EDIPA: Koma ine ndili ndi tsoka lalikulu! Zikhoza kuthekatu kuti ndina-
kwaniritsa ulosi wochititsa mantha uja mosazindikira.
YOKASI: Mukutanthawuza chiyani mbuyanga? Zimene mwayamba ku-
chitazitu zayamba kundichititsa mantha?
EDIPA: Nanenso ndili ndi mantha aakulu kwambiri. Komabe, ndikuga-
niza kuti ndikhoza kudziwa zowona zake ngati utandiyankha funso
linanso limodzi.
YOKASI: Nanenso ndasokonezeka maganizo, komabe funsani.
EDIPA: Kodi pawulendowo Layasi anapita ndi anthu ochepa kapena
anapita ndi gulu la asilikali monga zimakhalira ndi mfumu?
YOKASI: Anapita ndi amuna asanu, kuphatikizapo nthenga m’modzi.
EDIPA: Kalanga ine! Zonse zimene ukunenazo ndi zowona. Ndi ndani
anakuwuza zimenezi?
YOKASI: Wantchito wa Layasi, yemwe anapulumuka pachiwembucho.
EDIPA: Watchitoyo amakhala kuti? Amagwirabe ntchito m’nyumba
yathuyi?
YOKASI: Ayi. Atangobwera n’kumva zoti inuyo mwalongedwa ufumu
m’malo mwa Layasi, anandichonderera kuti ndimulole achoke kuno.
Ankati ndimutumize kubusa azikaweta nkhosa zathu. Iye sankafunanso
kukhala pakati pa anthu a ku Thebesi kuno. Nditawona chisoni chimene
anali nacho, ndinangomulola kuti achite zimene ankafunazo. N’zowona
kuti anali kapolo, koma zomwe anachita zinandikhudza kwambiri, moti
ndinamuchitira chifundo. Ndimawona kuti ankafunika kumuchitiranso
zoposa pamenepo.
EDIPA: Ndikufuna abwere kuno msanga, muyitanitse abwere pompa-
26