Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 30

Sewero la Mfumu Edipa YOKASI: Chabwino, basi ingoyimwerani madzi nkhani imeneyi. Musa- dere nkhawa za aneneri omwe amati akakhuta amayamba kuyankhula zinthu zosadziwika bwinobwino. Palibe munthu amene amalosera zolo- ndola. Aneneri a masiku ano ndi amabodza kwabasi. Ndikunena zime- nezo chifukwa cha ulosi wina womwe mneneri wina anatiwuza m’mbu- yomo. Ankati ulosiwo wachokera kwa Apolo. Ulosiwo unkati Layasi adzaphedwa ndi mwana wake, koma pamapeto pake zinapezeka kuti anaphedwa ndi achifwamba kudziko lina. Zimamveka kuti anaphedwa pamene panakumana misewu itatu kudziko lakutali. Komanso kuwonje- zera apo, mwana wathuyo atangobadwa n’kutha masiku atatu okha, La- yasi anamubowola mapazi n’kutuma wantchito kuti akamutaye kuma- piri. Choncho mapulani onse a Apolo analowa m’madzi ndipo ulosiwo unalephereka mochititsa manyazi. Pambuyo pake tinazindikira kuti ti- nkangochita mantha ndi nthano zachabechabe. Linali bodza lofuka utsi. EDIPA: Mkazi wanga, mawu amene wanenawa asungunuliratu mtima wanga, ndipo mutu wanga sukugwiranso . . . YOKASI: Bwanjinso? N'chifukwa chiyani mukuda nkhawa ndi zimene- zi? Nanga pali chodetsa nkhawa pamenepa? EDIPA: Si wanena kuti Layasi anaphedwa ndi achifwamba kudziko lina? YOKASI: Zimenezo ndi zimene tinamva ndipo anthu amakhulupirira kuti ndi zimene zinachitikadi. EDIPA: Zimene ukunenazo zinachitikira kuti? YOKASI: Pamalo ena otchedwa Fosisi. Zimamveka kuti pamalo amene- wo panakumana misewu itatu ndipo wina umapita ku Defi, wina uma- choka kuno, pomwe wina umapita ku Dawuliya. EDIPA: Zinachitika liti zimenezi? YOKASI: Zinachitika mutangotsala pang’ono kubwera kuno n’kulonge- dwa ufumu. EDIPA: Oo, mulungu wathu Zeu, n’chifukwa chiyani munalemba kuti ndidzakumane ndi tsoka lotere? YOKASI: Ukudandawula chiyani mwamuna wanga? N’chiyani chomwe chili chodetsa nkhawa pamenepa? 25