Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 29
Sewero la Mfumu Edipa
YOKASI: Inde, ndiwaperekeza ndikadziwa chimene chadzetsa mpu-
ngwepungwewu.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Amakambirana zinazake, ndiye
zinangopezeka kuti ayamba kukangana. Ndikuwona kuti zimenezi za-
chitika chifukwa sakumvetsetsana.
YOKASI: Onse awiri?
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Inde.
YOKASI: Chatsitsa dzaye n’chiyani?
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Ndi mavuto akuchitikawa, ndi-
kuwona kuti ndi bwino nkhaniyi tingoyisiya.
EDIPA: Wawonatu kuwopsa kwa nkhaniyi, si choncho? Ukuzindikira
zimenezi utandifowoketsa kale kuti ndisapereke chilango kwa munthu
amene akufuna kundipha.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Mbuyanga mfumu, ndanena ka-
le mobwerezabwereza kuti kungakhale kupanda nzeru kuyamba kuli-
mbana nanu kapena kukugalukirani. Inuyo munatipulumutsa mzinda-
wu uli pamavuto adzawoneni ndipo zinthu zinayamba kuyenda bwino.
Timakudalirani kwambiri ndipo timawonani monga mpulumutsi wathu.
YOKASI: Chonde mbuyanga, ndiwuzeni chimene chachititsa kuti mupse
mtima chonchi.
EDIPA: Iweyo mkazi wanga ndimakudalira kuposa anthu enawa. Ndiye
ndikuwuza chilungamo. Vuto ndi Kireyo. Kireyo akundikonzera chiwe-
mbu.
YOKASI: Ndiye n’chiyani chinachititsa kuti mufike pokangana choncho?
Tandiwuzeni zonse.
EDIPA: Kireyo amanena kuti ineyo ndi amene ndinapha Mfumu Layasi.
YOKASI: Anakuwuzani kuti wachita kumva nkhaniyi kwa winawake,
kapena anakuwonani mukuchita zimenezi.
EDIPA: Ayi, anagwirizana ndi mneneri wonyenga uja kuti adzandiwuze
zimenezi. Ndiye wabwera pano n’kuyamba kuwusasa mlanduwu ngati
kuti m’manja mwake ndi moyera.
24