Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 28
Sewero la Mfumu Edipa
mana ndi tsoka lowopsa ngati akunama.
EDIPA: Ndikuganiza kuti pofika pano umayenera kukhala ukudziwa
chimene ukupempha. Iwetu ukupempha kuti ineyo ndithamangitsidwe
kuno kapena ndiphedwe.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Ayi, ayi mbuyanga. Pamaso pa
Apolo, ndikunenetsa kuti ineyo ndife imfa yopweteka, milungu indifu-
latire komanso anzanga andisiye ngati ndanena zimenezi ndi maganizo
oyipa. Chimene chikundidetsa nkhawa kwambiri ndi mavuto amene
adzadza kunowa. Pamwamba pa mavuto amenewa, chinanso chomwe
chikundibalalitsa maganizo ndi mikangano yanuyi, yomwe ikungochi-
titsa kuti tizingovutikiravutikirabe.
EDIPA: Basi sindimuchita chilichonse ngakhale zili zowonekeratu kuti
ineyo ndiphedwa kapena kuthamangitsidwa mochititsa manyazi mu-
mzinda muno. Zimene wanenazi zandikhudza kwambiri ndipo ndichita
mogwirizana ndi mawu ako. Koma dziwa kuti sindikuchita zimenezi
chifukwa cha zimene Kireyo wanena ayi. Ndiye kuli bwino tsopano
achoke pano apite kunyumba kwake, chifukwa akakhalabe pano achiti-
tsa kuti mtima wanga uzingobwadamuka.
KIREYO: Koma ndinu wowuma khosi kwabasi. Ndikudziwa kuti muku-
chita zimenezi mokakamizika. Komanso ndi mtima wanu wapachalawo,
mukakwiya aliyense amavutika. Komanso mumamva zanu zokha. Simu-
funanso kuvomereza zomwe mwalakwitsa, zotsatira zake mumalephera
kuwona zinthu moyenera.
EDIPA: Zipita iwe! Kodi ndiwe gonthi? N’chifukwa chiyani ukukakami-
rabe kukhala pano?
KIREYO: Chabwino ndikupita. Zikuwoneka kuti sumunayambebe ku-
ndimvetsa. Koma anthu ali apawa akudziwa kuti ndine munthu wosala-
kwa.
[KIREYO akuchoka panyumba yachifumu ndipo akusiya EDIPA ndi YOKASI
komanso GULU LA ANTHU lija.]
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Adona, kodi mungawaperekeze
amfumuwa m’nyumba?
23