Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 27

Sewero la Mfumu Edipa akubwera moti mungachite bwino kudula kaye mkangano wanuwu. [YOKASI akufika kuchokera m'nyumba yachifumu.] YOKASI: Kodi n’chifukwa chiyani anthu akuluakulu ngati inu mukuka- ngana ngati ana? Simukuwona kuti dziko lanuli lawola ndi mavuto? Zo- wona simungachite manyazi kumakokanakokananso nokhanokha? A Edipa, kaloweni m’nyumba. Nawenso Kireyo zipita kwanu. N’chifukwa chiyani mukutibowola m’makutu ndi nkhani zanu zopanda ncherezi? KIREYO: Chemwali, mwamuna wanuyu akundiyimba mlandu wowo- psa kwambiri. Akuti akufuna kundithamangitsa kuno, apo ayi akuti andinyonga. EDIPA: Sakunamayi. Mkazi wanga, ndapeza kuti munthu uyu akundi- konzera chiwembu. Wayamba kugwirizana ndi anthu ena kuti andicho- tse pampando. KIREYO: Ndikunenetsa pano kuti ndikhale wotembereredwa ngati zi- mene akundinenezazi zilidi zowona. YOKASI: A Edipa, pamaso pa milungu yathu ndikukupemphani kuti mumukhulupirire mlamu wanuyu. Ngati wafika podzitemberera cho- nchi ndiye kuti sakunama. MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Zowonadi, chitani momwemo ndithu mbuyanga. Mawu amene mkazi wanuyu wanena ndi owona. EDIPA: Ndiye iweyo ukufuna kuti ineyo nditani? MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Perekani ulemu umene Kireyo akuyenera kulandira. Iyeyu sanayambe wakugalukiranipo ndi kale lo- nse, komanso lumbiro wachita lija ndi loti munthu sangalinene ndi milo- mo yabodza. EDIPA: Koma ukudziwa chimene ukunena iwe? MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Inde, ndikudziwa mbuyanga. EDIPA: Ndiye ndiwuze mosapita m’mbali chimene ukufuna ndichite. MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Simukuyenera kuyimba mlandu mnzanu wapamtima chifukwa cha mphekesera zopanda umboni. Pope- za mwamumva akulumbira, muyenera mukudziwa kuti akhoza kuku- 22