Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 26
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Ngati munthu wina akufuna kundiwukira kapena kundipanga
chipongwe, ndiyenera kudziteteza. Mmene anthu oyipa mitima akuchu-
lukira masiku ano mpofunika kumakhala osamala. Ukapusa ukhoza ku-
ngozindikira thupi lako lalowa m’bokosi.
KIREYO: Ndiye mukufuna munditani, mundithamangitse kuno?
EDIPA: Ayi. Ndikufuna kuti ufe n’cholinga choti ena atengerepo phu-
nziro kuti aziganiza kawiri asanayambe kuchitira anzawo nsanje kapena
kaduka.
KIREYO: Mwatsimikizadi mtima moti simusintha maganizo?
EDIPA: Iweyo sungasinthe maganizo anga ndipo sindingayerekezenso
kukhulupirira zonena zako. Kukhulupirira munthu ngati iweyo n’chi-
modzimodzi kuyika mutu wanga mkamwa mwa ng’ona.
KIREYO: Ndikuthadi kuwona kuti panopa simukuganiza bwino.
EDIPA: Ndikuganiza bwinobwino bwanawe, moti usanganize kuti ndi-
kucheza ayi. Ndikufuna kuteteza moyo wanga.
KIREYO: Komatu mukufunikanso kuteteza ineyo.
EDIPA: Nditeteza bwanji munthu wosakhulupirika ngati iwe, munthu
yemwe umandisekerera kuseri ukundinolera lupanga loti undibaye
nalo? Khalidwe lako ndi lochititsa nseru kwabasi.
KIREYO: Koma nanga bwanji ngati mukulakwitsa?
EDIPA: Ngakhale zitakhala kuti ndikuphonya, zomwe ndagamulazi sizi-
ngasinthe.
KIREYO: Komatu zinthu sizikutherani bwino ngati mwayamba kulamu-
lira mopanda chilungamo choncho.
EDIPA: Ayi, Thebesi yense ali m’manja mwanga. Palibe amene angandi-
wopseze kapena kundiwuza zochita.
KIREYO: Komatu inenso ndi mzika ya Thebesi ndipo ndine mfulu ngati
inuyo. Si ine kapolo wa munthu kuti mundichitire zopanda chilungamo
chonchi.
[Khomo la nyumba yachifumu likutsegulidwa.]
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Pepani olemekezeka, Yokasi
21