Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 25

Sewero la Mfumu Edipa chimene ndikufuna kuchokera kwa inuyo ndipo sindikhala ndi mantha aliwonse pochita zimenezi. Ndikanakhala mfumu, bwenzi ndikukaka- mizika kumachita zinthu zimene sindikufuna. Kunena zowona, ndima- wona kuti kukhala mfumu ndi chintolo chachikulu kwambiri moti udi- ndo ndili nawowu ndimakhutira nawo. Ineyo sindiwona kuti ndi nzeru kumafuna chinthu chomwe chikhoza kungondibweretsera mavuto. Pa- nopa anthu amandipatsa ulemu wondiyenerera ndipo ndimasangalala ndi zimenezi. Anthu amene akufuna kuti muwachitire zinazake amata- manda ine, chifukwa inuyo mumatuma ine kuti ndikachite zinthuzo m’malo mwanu. Akawona kuti ndikuchitapo kanthu ndi ine, amayamba kuwona kuti wabwino ndine osati inuyo. Ndiye ndingachitirenji zopa- nda nzeru potaya mwayi umenewo n'kukhala mfumu? Munthu woga- niza bwinobwino sangachitenso chiwembu pamenepo. Ndikukutsimi- kizirani kuti ine ndilibe mtima umenewo. Ndipo ngati wina atayamba kuchita chiwembu chamtundu umenewo, ine sindingamutsate kapena kumuthandiza. Ngati mukufuna kutsimikizira zimenezi, pitani ku Defi. Mukakafika kumeneko kafunseni mneneri wa Apolo. Zimene atakaku- wuzeni mukaziyerekezere ndi zimene ndanenazi muwone ngati ndi- kunama. Ngati mutapeza kuti ndimakonzadi chiwembu mogwirizana ndi a Teresi, mudzandikwidzinge ndi unyolo n'kundidula mutu. Sikuti mudzachite zimenezi kokha chifukwa choti ndapalamula mlandu, koma chifukwa choti inenso ndingakonde kulandira chilango chomwecho ndi- tadzigwira ndikuchita chinyengo chotere. Choncho ndikukupemphani kuti musapitirize kundiyalutsa pagulu ngati pano pondiyimba mlandu wopanda umboni ngati umenewu. Sichilungamo kumaweruza munthu chifukwa chongomuganizira kuti wachita zinazake. Ineyo, ndimawona kuti munthu amene akutaya mnzake wokhulupirika chifukwa cha mphekesera amakhala ngati akutaya moyo wake weniweniwo. Ingode- khani pang'ono, muyamba kuwona zinthu moyenera nthawi ikamapita. Pajatu amati nthawi imayesa zonse. Nthawi imafukula ngakhale mabo- dza akuluakulu. Nayenso munthu amene akuchita zoyipa tsiku limadza- mukwanira ndipo amadzawonekera pambalambanda n’kuyaluka. MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Ngati Kireyo wafika ponena mawu amenewa ndiye kuti sakunama. Munthu amene akunena bodza sangafike polumbira komanso kudzitemberera choncho. 20