Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 24
Sewero la Mfumu Edipa
kuti mundiyende pansi, si bwenzi atanena kuti ineyo ndi amene
ndinapha Mfumu Layasi.
KIREYO: Koma ngati ananena zimenezo, inuyo ndi amene mukudziwa
chilungamo chake. Tsopano yafika nthawi yoti nanenso ndikufunseni
mafunso.
EDIPA: Funsa, palibe amene wakutseka pakamwa. Koma ngati ukuwe-
rengera kuti upeza kuti ineyo ndi amene ndinapha Mfumu Layasi ndiye
ukungotaya nthawi yako.
KIREYO: Chabwino, ndiyankheni kaye funso langali: Kodi inuyo muna-
kwatira mchemwali wanga?
EDIPA: Ngakhale kuti ukufunsa chinyezi kubafa, ndikuyankha. Inde,
ndinakwatira mchemwali wako.
KIREYO: Ndipo nonse awiri mumalamulira ndi mphamvu zofanana
mumzindamu, si choncho?
EDIPA: Inde, chilichonse chimene mkazi wanga akufuna ndimamupatsa
mosawumira.
KIREYO: Ndipo ineyo ndimalamulira ndi mphamvu zofanana ndi awi-
rinu, si choncho?
EDIPA: Chimenecho n'chifukwa chake ndinanena kuti kusakhulupirika
wachitaku n'kowopsa kwambiri. Sindikumvetsa kuti wachitadi zimenezi
ndikaganizira kuti ndiwe m'bale wanga komanso mnzanga wapamti-
ma!
KIREYO: Komatu zinthu sizili choncho, moti mutaganiza bwinobwino,
muwona kuti mukuphonya kwambiri. Choyamba, taganizirani izi: Kodi
mukuganiza kuti munthu angasankhe chiyani pakati pa kukhala wola-
mulira n'kumavutika ndi nkhawa, ndi kukhala pansi pa ulamuliro wa
munthu winawake n'kumasangalala ndi mtendere wam'maganizo ko-
manso ufulu, koma ali ndi mphamvu zofanana ndi zimene akanakhala
nazo akanakhala wolamulira? Ndikukuwuzani kuti ineyo sindimafuna
kukhala mfumu. Ndimasangalala kumagwira ntchito zina zaboma. Ndi-
kuwonanso kuti munthu aliyense amene mutu wake umagwira bwino-
bwino angaganizenso mofananamo. Panopa ndimapeza chilichonse
19