Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 23
Sewero la Mfumu Edipa
kitsa kuti ndiyitanitse Teresi?
KIREYO: Inde, ndinaterodi. Ndipo mukanakhala kuti simunamuyitane
ndikanakulimbikitsaninso kuchita zomwezo.
EDIPA: Kodi patenga nthawi yayitali bwanji kuchokera pamene Mfumu
Layasi . . . [Ak uyim a k aye .]
KIREYO: Mfumu Layasi yatani? Kodi nkhaniyi ikumukhudza bwanji
Layasi?
EDIPA: Usandidule pakamwa. Ndafunsa kuti patenga nthawi yayitali
bwanji kuchokera pamene Mfumu Layasi inachoka kuno n'kukaphedwa
ndi achifwamba?
KIREYO: Zinachitika kale kwambiri. Padutsa zaka zambirimbiri.
EDIPA: Kodi pa nthawi imeneyo, Teresi anali mlosi wodalirika ngati
mmene alili masiku ano?
KIREYO: Inde, sanasinthe ngakhale pang’ono.
EDIPA: Ndiye tandiwuze, Teresi anayamba waloserapo zokhudza ine?
KIREYO: Ayi, sanayambe wakutchulanipo, kusiyapo ngati ananena zi-
menezo ine palibe.
EDIPA: Mutamva zoti Mfumu Layasi yaphedwa, kodi munayamba kufu-
nafuna anthu amene anapha mfumuyo?
KIREYO: Inde, tinayamba kufufuza. Koma sitinagwire munthu aliyense.
EDIPA: Ndiye n'chifukwa chiyani mlosi wanuyu sananenepo kanthu?
Bwanji sanakuthandizeni kupeza anthu omwe anapha mfumuyo?
KIREYO: Sindikudziwa. Ndikakhala kuti sindikudziwa zambiri zokhu-
dza nkhani inayake, ndimawona kuti ndi bwino kungotseka pakamwa
panga n’kukhala chete.
EDIPA: Koma uyenera ukudziwapo kanthu. Usandinamize kuti suku-
dziwa chilichonse. Ukuyenera kundiwuza . . .
KIREYO: Kukuwuzani chiyani? Ndikanakhala kuti ndikudziwapo ka-
nthu ndikanakutsanulirani zonse zimene ndikudziwa.
EDIPA: Ukunama iwe. Zikanakhala kuti Teresi sanapangane ndi iweyo
18