Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 22
Sewero la Mfumu Edipa
chifukwa nthawi zina zimene zimawoneka panja si zimene zimakhala
mumtima. Ubwino wake a Edipa ndi awo akubwerawo, mwina muwa-
funse akuwuzeni.
[EDIPA akutuluka kuchokera m'nyumba yachifumu.]
EDIPA: Iwe, ndi ndani wakulola kufika kuno? Kodi watha mantha kuti
tsopano ufike pobwera kunyumba kwanga kuno? Ndiwe munthu amene
unapha mwini nyumbayi, ndpo zikuwoneka kuti ukufunanso kulanda
ufumu wanga? Tabwera kuno undiyankhe, kodi unapangana ndi mne-
neri wabodza uja kuti azidzandiwuza phala lakelo poganiza kuti mu-
ngandipite pansi? Kapena umaganiza kuti sindizindikira kuti ndiwe
tambwali wotheratu yemwe amakhala ngati nkhosa pamaso, mumtima
ali m’mbulu wolusa? Kodi zimene ukuyesa kuchitazi ukuganiza kuti
zikakufikitsa kuti? Pa moyo wanga sindinayambe ndawonapo munthu
wopanda manyazi ngati iwe. Zowona ukuganiza kuti ungalande mpa-
ndo wachifumu mophweka choncho?
KIREYO: Bwanji mumve kaye mbali yanga musanathe mawu?
EDIPA: Ukufuna udziyikire kumbuyo. Ngati ukuganiza kuti ungandi-
pusitse ndiye walemba m’madzi. Sungasunthe mtima wanga ndi paka-
mwa pako pathererepo. Chomwe ndikudziwa n’choti ndiwe tambwali
wotheratu, munthu amene amandimwetulira akundisungira kampeni
kumphasa.
KIREYO: Chonde yambani mwandimvetsera kaye.
EDIPA: Palibenso chimene ungandiwuze, ndiwe munthu wosakhulupi-
rika ngakhale pang’ono.
KIREYO: Ngati mukuganiza kuti kuvuta kumasonyeza nzeru ndiye kuti
nzeru zanu zatayika. Simukuyenera kumaganiza choncho.
EDIPA: Nawenso ngati ukuganiza kuti ukhoza kundikonzera chiwembu
n’kuzemba chilango, ndiye ukudzinamiza. Iwenso sukuyenera kumaga-
niza choncho.
KIREYO: Zowonadi. Zimene mukunenazo ndi zowona. Ndiyetu ndiwu-
zeni mlandu umene mukunena kuti ndapalamulawo!
EDIPA: Unditsutse ngati ndikunama, kodi iweyo si amene unandilimbi-
17