Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 21
Sewero la Mfumu Edipa
ngakhale kuti panopa akuwona bwinobwino. Akhala mphawi wothe-
ratu, ngakhale kuti panopa ndi wokhupuka. Komanso achoka mumzi-
nda uno n'kukakhala mlendo kudziko lakutali akupapasa njira ndi ndo-
do yake. Akamachoka kuno akhala atazindikira kuti ana ake enieni ndi
azichimwene komanso azichemwali ake. Azindikiranso kuti mkazi wake
ndi mayi ake omubereka. Munthuyo anapha atate ake n'kukwatira mayi
ake n’kubereka nawo ana. Pitani m’nyumba mwanu mukaganizire mo-
zama ndagi imeneyi. Mukapeza kuti zimene ndanenazi ndi zabodza,
mubwere mudzandiwuze ndipo ine nditula pansi udindo wanga monga
mneneri.
[TERESI akunyamuka akutsogoleredwa ndi MNYAMATA. EDIPA akutembe-
nuka n'kukalowa m'nyumba yachifumu. Kenako KIREYO akutulukira n'kuya-
mba kuyankhula ndi gulu la anthu lija.]
KIREYO: Inu mzika za ku Thebesi, ndangomva zoti mfumu yathu yane-
na kuti ineyo ndikuyikonzera chiwembu. Kunena zowona ine sindinga-
chite zimenezo, moti ndabwera pano kuti ndidzikanire pamaso panu.
Ndi zimene zikuchitikazi, ngati a Edipa akukhulupirira kuti mavutowa
akuchitika chifukwa cha ine, ndikunena pano kuti asalole kuti ndikhale
ndi moyo wawutali. Ndithu anditsitsire kumanda m’mutu mwanga
musanadzadze imvi. Ndikudandawula kwambiri kuti andiwonongera
mbiri yanga asanatsimikizire kuti ndinedi wolakwa.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Komatu n’kutheka kuti akupa-
kani mlanduwu chifukwa chopsa mtima. Ine ndimawona kuti munthu
akapsa mtima mnzeru zimamuthawira, moti ndikukupemphani kuti
musaganizire kwambiri mawu amene anena.
KIREYO: Komatu ndamva zoti amanena kuti ineyo ndawapita pansi
n'kupangana ndi Teresi kuti adzawawuze zabodza!
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Anaterodi, koma n’kutheka kuti
amanena zimenezo asakuganiza bwinobwino.
KIREYO: Mwati amanena zimenezi atakwiya?
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Zikuwoneka kuti anali atakwiya
kwambiri. Komabe tisadalire kwambiri zimene tangowona ndi maso
16