Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 20
Sewero la Mfumu Edipa
TERESI: Inetu sindimafuna kubwera kuno, inuyo ndi amene munatuma
munthu kuti adzanditenge.
EDIPA: Kungoti sindimadziwa kuti mudzayankhula zopusa chonchi.
Ndikanadziwa sindikanayerekeza n’komwe.
TERESI: N’zowona kuti ndinabadwa wosawona. Koma musaganize kuti
ndinachita kufuna. Ndipo ndikuwuzeni pano kuti makolo anu sankawo-
na chilema changachi ndipo ankandilemekeza kwambiri.
EDIPA: Mwati chiyani? Makolo anga? Mumawadziwa makolo anga inu?
TERESI: Dikira ndikuwululireni chinsinsi chonse bwinobwino ndipo
chinsinsi chimenechi n’chimene chitakuwonongeni kotheratu.
EDIPA: Chakudzerani n’chiyani a Teresi? Mwakhuta chiyani lero? Bwa-
nji mukungoyankhula chipwitikizi chokhachokha? Mukuganiza kuti
ndinakuyitanani kuti tizidzachita ndagi?
TERESI: Pajatu inu ndi katswiri wodziwa kupereka mayankho a ndagi
zovuta kwambiri, moti ndikulakalaka muyankhe ndagi ndaperekayi.
EDIPA: Inutu mwatumidwa! Tiyeni nazo, muwona kuti palibe amene
angasewere ndi ine.
TERESI: Nzeru zanuzo ndi zimene zitakuwonongeni.
EDIPA: Ndilibe nazo ntchito! Tiwona amene atawonongeke.
TERESI: Basi ndilekeni ndizipita kwathu ine. Mnyamata, ndilondolere
njira!
EDIPA: Inde, akufunikadi akulondolereni njira. Mukakhalabe pano mu-
ngotiphulitsapo ngozi.
TERESI: Koma ndisanapite ndikufuna ndikuwuzeni kaye chimene chi-
nandichititsa kuti ndibwere ngakhale sindimafuna. Ineyo sindikuchita
mantha ndi nkhope yanu yokwiyayo chifukwa palibe chimene munga-
ndichite. Ndakuwuzani kale kuti, munthu amene mwakhala mukumu-
funafuna nthawi yonseyi ali pompano. Malinga ndi zimene ndikudziwa,
munthuyo ndi mlendo amene amakhala kuno. Koma mukafufuza mupe-
za kuti si mlendo ayi. Ndi mbadwa ya ku Thebesi konkuno. Munthuyo
akangozindikira zimenezi moyo wake uwonongekeratu. Achita khungu,
15