Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 19
Sewero la Mfumu Edipa
TERESI: N’zowona kuti inuyo ndi mfumu yathu, komabe musayiwale
kuti nanenso ndili ndi ufulu wokuyankhani. Ndili ndi ufulu wochita
zimenezi chifukwa si ine kapolo wanu. Ine ndimatumikira Apolo, ndipo
sindingagwirizane ndi Kireyo kuti ndikukonzereni chiwembu. Choncho
mawu anga kwa inu ndi awa: Mwandisambula pagulu ngati pano po-
nyoza chilema changa. Komatu musamayiwale kuti lungalunga m’poba-
dwa, chilema chichita kudza usana. N'zowona kuti muli ndi maso, maso
akenso akuluakulu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti simutha kuwona zi-
nthu zosaneneka zimene mukulakwitsa, makamaka kunyumba kumene
mukukhalako komanso anthu amene mumakhala nawo limodzi. Kodi
mumalidziwa bwinobwino banja limene munachokera? Mwachimbuli-
mbuli munadzisandutsa kukhala mdani wa abale anu enieni, ndikune-
nanso za ena omwe ali pansi panthakapa, komanso amene adakali mo-
yo. Ndipo ndi miyendo iwiri ya ulosi wopatsa mantha womwe unapere-
kedwa kwa makolo anu, muchoka kuno mukulira. Ulosi wangati the-
mberero umenewu umangokhala ngati mpeni wakuthwa konsekonse
womwe unawacheka makolo anu pakhosi, ndipo ukuchekaninso inuyo
mopanda chisoni n'kuchititsa kuti muyingitsidwe ngati ntchentche. Ma-
so anuwo, omwe tsopano akuwala ndi umoyo, achita mdima. Aliyense
amva kufuwula kwanu mukangodziwa zowona zenizeni za ukwati ume-
ne unachititsa kuti mukhale pampando wachifumuwo. Unalidi uleme-
rero wawukulu kukhala pampando umenewo, koma simunkadziwa
ululu wowopsa umene ulemererowo unkakusungirani. Posachedwapa
mavuto ochuluka azinga inuyo limodzi ndi ana anu. Ndiye mukhoza
kupitiriza kundinyoza komanso kutukwana Kireyo. Mukhozanso ku-
nyoza ulosi wangawu. Koma dziwani kuti padziko lonse lapansili, kuvu-
ma komanso kuzambwe, palibenso munthu wina yemwe atawononge-
dwe mopweteka kwambiri ngati inuyo.
EDIPA: Mwano umene mwayankhulawu wandikwana. Ndichokereni
pano msanga musanandiphulitse ngozi. Ndikungopempherera kuti
mliri wavutawu udziwe nanu chochita. Kumanda kukanati kudzisankha
tikanayamba tatumiza kaye enanu, n’kusunga ena aphindu omwe anga-
tukule mzinda wathuwu. Ndati ndichokereni! Tembenukani mudzipita
kwanu ndipo musadzapondenso pakhomo panga pano.
14