Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 18
Sewero la Mfumu Edipa
Bwanji mumangokhala ngati matupi anu anapangidwa ndi nsanje yo-
khayokha. Mukufuna mundichotse pampando n’cholinga choti mukha-
lepo. Inetu sindinachite kuwumiriza anthu kuti andilonge ufumu. Okha
anachita kundikakamiza atawona ntchito zanga zakupsa. Ndakhumu-
dwa kwambiri kuzindikira kuti Kireyo, mnzanga komanso m’bale wa-
nga weniweni, akundikonzera chiwembu kuti andichotse pampando
ndipo wagwirizana ndi wansembe wachinyengoyu, yemwenso ndi wo-
sawona kotheratu kuti andiwukire. Wansembe yemwe ndi khungu la-
kelo amangowona zinthu zokhazo zomwe zingamupindulitse. Ngati
akutsutsa zimene ndikunenazi andipatse umboni womveka bwino. Ndi-
po inuyo monga wansembe, kodi munali kuti pamene chilombo choyi-
mba chija chinkazunza komanso kupha anthu kuno? Palibetu munthu
amene ankadutsa pamaso pake popanda kupereka yankho lolondola la
ndagi yake ija ndipo ambiri anadibwa chifukwa chochita masewera
amenewa. Koma inuyo simunanene chilichonse kuti muwapulumutse.
N’chifukwa chiyani sumunawathandize kupereka yankho lolondola la
ndagiyo? N’chifukwa chiyani anthu sanabwere kwa inu monga mneneri
wawo kuti muwathandize? Anthuwotu ankadziwa kuti ndinu mneneri
wopanda phindu, yemwe amangodendekera mutu wake n’kumanamiza
anthu kuti amawona zinthu zomwe ena sangaziwone chonsecho maso
ake ndi akhungu. Koma tawonani ineyo munthu yemwe sindinkadziwa
chilichonse, ndinabwera kuno n’kugonjetsa chilombocho ndi nzeru za-
nga popanda kudalira mbalame zolosera. Anthu atawona ubwino wa-
nga, anandilonga ufumu. Ndiye lero mungodzuka uko, manthongo ali
bwito-o m’manso, nkhongo zili gwa, n’kumanena kuti ndine amene
ndinapha Layasi, zachamba eti! Kuteroko mukuwerengera kuti Kireyo
akakhala mfumu adzakupatseni mpando wonona kuti muzidzadya
bwino? Chomwe ndikudziwa n’choti nonse munong’oneza bondo ndi
zimene mukuchitazi. Zikanakhala kuti si inu wokalamba chonchi, bwe-
nzi mutalandira chilango chokhwima kwambiri kuti mutengerepo phu-
nziro.
WOTSOGOLERA GULU LA ANTHU: Kwa ifeyo, zikuwoneka kuti a
Teresi ayankhula chifukwa chopsa mtima. Nayonso mfumu yathu Edipa
yayankhula mtima ukuwawa. Mapokoso amenewa satithandiza kupeza
njira yothetsera mavutowa.
13