Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 17
Sewero la Mfumu Edipa
mene mwanena.
TERESI: Ndanena kuti munthu amene mukumufunafunayo sali kutali
ayi, ndi inu nomwe!
EDIPA: Kameneka ndi kachiwiri kunena bodza loyipali, lomwe likhoza
kukulowetsani m’mavuto owopsa.
TERESI: Mukufunanso ndikuwuzeni zambiri kuti mukwiye zenizeni?
EDIPA: Mukhoza kuchita zimene mukufuna.
TERESI: Ndikunenazi ndi zowona, kungoti inuyo simukudziwa. Moyo
umene mukukhala ndi wochititsa manyazi kwambiri. N’zomvetsa chiso-
ni kuti ngakhalenso banja lanu silikudziwa.
EDIPA: Mukuganiza kuti munganyazitse mfumu n’kungosiyidwa ulele?
TERESI: Ngati chowonadi chilidi champhamvu palibe chingandichiti-
kire.
EDIPA: Chowonadi chilidi ndi mphamvu, koma osati kwa anthu ama-
bodza ngati inuyo. Inuyo mulibe chowonadi ngakhale kadontho chifu-
kwa zonse, kuyambira makutu, maganizo komanso maso anu, ndi zaku-
fa. Zinafa kalekale.
TERESI: Komatu mukuchitaku ndi kusaganiza bwino, chifukwa mawu
oyipa mukundinenerawa akutembenukirani.
EDIPA: Sindikuwopa zimenezo. Ndi maso anu amdimawo simungakwa-
nitse kulimbana nane. Ngakhale munthu amene amawona bwinobwino
sangalimbane ndi ine. Ndiye kuli bwanji wopanda maso ngati inu!
TERESI: Ndikunenazi ndi zowona ndithu. Ndipo musade ine chifukwa
si ine amene ndachititsa kuti mukumane ndi tsoka limeneli. Muzimuyi-
mba mlandu Apolo.
EDIPA: Ayi musandinamize, Kireyo ndi amene wakutumani, n’zosathe-
ka kuti mungoyamba kunena zimenezi poyerayera.
TERESI: M’manja mwa Kireyo ndi moyera. Mavutowa munawapalamu-
la nokha bambo.
EDIPA: Anthu inu ndi oyipa kwabasi. Munthu asalemere ayi, asakhale
mfumu kapena kukhala ndi luso linalake koma kumuchitira nsanje basi.
12