Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 16
Sewero la Mfumu Edipa
TERESI: Ngakhale mukunena kuti ndine wodzikonda, dziwani kuti
inuyo ndi amene mukulephera kuwona kudzikonda kumene muli nako.
Koma n’zomveka, paja chala sichiloza mwini!
EDIPA: Ndi munthu wamtundu wanji amene angapitirize kumvetsera
zimenezi osapsa mtima. Musaganizetu kuti tidwala m’mimba chifukwa
choti simunatiwuze zimene mwawona.
TERESI: Inde simudwala. Komabe dziwani kuti chinsinsi chimenechi
chikatumbuka chikubowolani m’mimba.
EDIPA: Ndiye popeza mwati chitumbuka, ndiye bwanji osangonena?
TERESI: Pepani kwambiri. Akuluakulu anati, ukayenda siya phazi, uka-
siya mulomo umakutsata.
EDIPA: Ndinu munthu wosathandiza ngakhale pang’ono, moti mwa-
ngotitayitsa nthawi yathu yamtengo wapatali. Ndikutha kuwona kuti
nanunso munatengapo mbali pachiwembuchi. Mwinanso n’chifukwa
chake simukufuna kuyikapo mlomo.
TERESI: Mwatero? Inutu mukungofuna kundiyankhulitsa pambali! Zi-
kanakhala kuti ndinakonza nawo chiwembucho ndikanakuwuzani kuti
mundiphe. Mwina ndikumasuleni tsopano, munthu amene akuchititsa
kuti mzindawu uthimbirire mpaka milungu kukwiya ndi inuyo.
EDIPA: N’chifukwa chiyani mukuyankhula zoduka mutu? Mukuganiza
kuti mungayankhule mawu amenewa osalangidwa? Dikirani muwone.
TERESI: Inetu sindilangidwa. Chowonadi n’chimene chinganditeteze.
EDIPA: Ndi ndani wakuwuzani zimenezi? Sizingatheke kuti mungo-
bwera pano n’kuyamba kundiloza chala.
TERESI: Inuyo ndi amene mwandiwuza. Pajatu ine sindimafuna kuya-
nkhula, koma mwachita kundikakamiza.
EDIPA: Mukutanthawuza chiyani?
TERESI: Muziyankhulatu chilungamo inu! Mukunenetsa kuti simuna-
mve zomwe ndanena zija? Kapena mukungofuna kunditapa mkamwa?
EDIPA: Sindikukuyesani. Ndafunsa chifukwa ndikufuna kumvetsa zi-
11