Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 15
Sewero la Mfumu Edipa
adzazimitsa zako.
TERESI: Mfumu yanga, inetu ndikusowa chonena! Kodi nzeru zinga-
khale zaphindu lanji ngati zitamubweretsera munthu mavuto? Ndisaku-
namizeni pano kuti sindimadziwa nkhaniyi. Ndimayidziwa ndithu, ku-
ngoti ndinasankha kungoyiponya kunkhongo. Musaganize kuti ndika-
nabwera kuno mukanapanda kutuma munthu kuti adzanditenge.
EDIPA: Bwanjinso, pali vuto kapena? N’chifukwa chiyani nkhope yanu
ikuwoneka yakugwa?
TERESI: Ngati n’zotheka, chonde ndiloleni kuti ndibwerere kwathu. Ti-
yeni tingokhutitsidwa ndi mavuto amene akuchitikawa m’malo moti ti-
zitokosolanso ena aphe-e.
EDIPA: Zimene mwanenazo si zolimbikitsa ngakhale pang’ono, koma-
nso zikusonyeza kuti ndinu munthu wodzikonda kwambiri.
TERESI: Nanunso zimene mwanenazo ndi zosalimbikitsa ngakhale pa-
ng’ono. Inetu sindikufuna kuyikapo mlomo pa nkhaniyi chifukwa sindi-
kufuna kuwonjezera mavuto alipo kalewa.
EDIPA: Ngati mukudziwa pomwe pagona vuto, bwanji osangonena? Zo-
wona mukufuna tichite kukunyambitani mapazi komanso kung’amba
kukamwa kuti mutiwuze?
TERESI: Inuyo mbuyanga mfumu ndinu munthu wosamva za ena.
N’chifukwa chiyani mukundikakamiza kuti ndikuwululireni chinsinsi
chowopsa ngati chimenechi, chomwenso chikhoza kukubweretserani
mavuto aakulu?
EDIPA: Mukutanthawuza chiyani? Mukufuna mundiwuze kuti simune-
na chilichonse ngakhale mzindawu uwonongeke?
TERESI: Ineyo sindikufuna kudzibweretsera mavuto kapena kukubwe-
retserani chisoni. N’chifukwa chiyani mukuvutika ndi nkhani imeneyi?
Palibetu chimene mutapindulepo.
EDIPA: Ndinu munthu wotembereredwa kwambiri! Anthu ngati inu
mukhoza kupsetsa mtima ngakhale mwala! Zowona mukukanika ku-
ngotiwuza zimene mulungu wakuwululirani? Koma ya-a! Anthu enadi
amakhala owuma mitima ngati mfiti.
10