Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 14
Sewero la Mfumu Edipa
EDIPA: Usadandawule, ndachita kale zimenezo. Kireyo anandiwuzanso
zomwezo moti ndatuma munthu kuti akamutenge. Ndikudabwa kuti
n’chifukwa chiyani sakutulukira mpaka pano?
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Kuwonjezeranso pamenepo, pali
mphekesera zinanso zokhudza nkhaniyi zomwe zinkamveka kalelo.
EDIPA: Mphekesera zake zotani? Ndikufuna kumva chilichonse chokhu
dza nkhani imeneyi.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Zimamveka kuti mfumu Layasi
inaphedwa ndi anthu apawulendo.
EDIPA: Enanso anandiwuza zimenezo, koma palibe amene ananditsimi-
kizira kuti ndi zowona.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Koma ndikuganiza kuti ndi ma-
temberero mwanena aja, munthu amene anachita zimenezi abwera poye-
ra, chifukwa akapanda kutero adzibweretsera tsoka lowopsa.
EDIPA: Komatu usayiwale kuti munthu akafika popha munthu mtima
wake umakakala moti samawopanso chilichonse.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Ndikudziwa, koma osati ngati
pali munthu yemwe akhoza kumubweretsa poyera. A Teresi ndi awo
akubwera apowo, mneneri wokhala ngati mulungu, yemwe amawona
zinthu zosawoneka ndi maso.
[Akulowa TERESI akutsogoleredwa ndi MNYAMATA.]
EDIPA: Takulandirani a Teresi, mneneri wathu. Timadziwa kuti ndinu
munthu wozindikira kwambiri. Mumadziwa zinthu zomwe palibe ame-
ne angazimvetse. Mumadziwanso ngakhale zinthu zomwe zimachitika
kumwamba. Ngakhele kuti ndinu wakhungu, ndikuganiza kuti muku-
dziwa bwino kuti dziko lathuli lawoleratu. Choncho takuyitanani kuti
mutithandize kumvetsa zimene Apolo wanena. Apolo akuti mliri wati-
gwerawu ukhoza kutha ngati titapeza anthu amene anapha Mfumu La-
yasi. Choncho tiwuzeni chimene mwawona kapena kumva kuchokera
kwa milungu. Chonde pulumutsani mzindawu komanso dzipulumitse
nokha potiwuza zolondola zokhudza nkhaniyi. Miyoyo yathu ili m’ma-
nja mwanu tsopano. Paja amati mnzako akapsa ndevu m’zimitse, mawa
9