Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 13
Sewero la Mfumu Edipa
wa ku Thebesi kuno ndi amene wandiwuza zimenezi ndipo n’kupusa
kwambiri kuchita zosemphana ndi zimene mulungu wanena. Choncho
ndikutemberera aliyense amene anapha Layasi kuti moyo wake usapeze
mtendere ngakhale pang’ono. Ndikupempheranso kuti aliyense amene
angalandire munthu wotero kunyumba kwake akumane ndi masoka
onse amene munthu amene anapha mfumuyi angakumane nawo. Nga-
khale zikanakhala kuti milungu sinatilamule kuchita zimenezi, timaye-
nerabe kuzichita. Timayenera kubwezera imfa ya mfumu yathu yomwe
inaphedwa yosalakwa. Ndiye popeza tsopano ndili ndi mphamvu zime-
ne mfumuyo inali nazo komanso ndinalowa m’nyumba yake n’kumube-
rekera ana, ndiwonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Ndimenya nkho-
ndo m’malo mwake. Ndichita zimenezi mofanana ndi zimene mwana
amachita pobwezera anthu amene anapha bambo ake. Kwa amene saku-
funa kutsatira zimene ndalamulazi, ndikupempha kuti milungu iwafula-
tire, nthaka yawo ikhale yosabala, akazi awo akhale osabereka, komanso
onse atikitidwe ndi mliri wagwawu. Koma nonse amene mutamvere
zimene ndakuwuzanizi, mtendere ukhale nanu ndipo milungu ikukhu-
thulireni madalitso.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Mbuyanga mfumu, popeza the-
mbereroli mwalilunjika kwa ine, ndikufuna ndikuwuzeni kuti ndinapha
Layasi si ine, komanso ndingakutsimikizireni pano kuti sindikudziwa
amene anamupha. Ngati mukufuna kudziwa amene anamupha munga-
chite bwino kukafunsa Apolo yemweyo, chifukwa ndi amene watakasa
nkhaniyi. Mwina angakakutchulireninso dzina lake.
EDIPA: Zimene wanenazo ndi zowona. Komatu palibe munthu amene
angakakamize mulungu kuti ayankhule asakufuna.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Kodi mungalole kuti ndikupa-
tseniko uphungu pang’ono?
EDIPA: Usachite mantha, yankhula.
MTSOGOLERI WAGULU LA ANTHU: Ine ndikudziwa kuti tili ndi
mneneri wathu kuno, yemwe amatha kuwona zinthu mofanana ndi mu-
lungu wathu Apolo. Bwanji osamufunsa ameneyo? Mwinatu akhoza
kukuthandizani kudziwa amene anapanga chiwembuchi!
8