Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 12

Sewero la Mfumu Edipa abwere kuno. Ineyo ndiyesetsa kuchita zonse zimene ndingathe kuti ndi- peze munthu amene anachita zimenezi n’cholinga choti zinthu ziyambi- renso kuyenda bwino. Chonde tiyeni tigwirane manja. Dziwani kuti ti- kapanda kutero tikhala pamoto wawukulu. [EDIPA ndi KIREYO akulowa m’nyumba yachifumu.] WANSEMBE: Tiyeni tinyamuke anthu inu, mfumu yathuyi yapereka ya- nkho la funso limene linatibweretsa kuno. Tiyeni tingopempherera kuti Apolo, yemwe watumiza uthegawu, atipulumutse kumavuto atifiyiritsa masowa. [WANSEMBE ndiponso MZIKA zonse zikuchoka. Panjapo patsala gulu la anthu omwe akupemphera kwa Zeu. Posakhalitsa EDIPA akutuluka kuchokera m’nyumba yachifumu n’kukayamba kuyankhula ndi anthu omwe asonkhana panja paja.] EDIPA: Siyani kaye kupempherako mundimvetsere. Ine ndili pano kuti ndikuthandizeni. Ineyo ndiyankhula monga munthu amene sindikudzi- wa nkhani yonse yokhudza chiwembu chinachikacho. Nditakhala kuti ndikufufuza ndekha anthu amene anapalamula mlanduwu, sindingapite patali chifukwa sindikudziwa zambiri zokhudza nkhaniyi. Ndikutero chifukwa mlanduwu unapalamulidwa ine ndisanabwere kuno. Choncho mawu anga ndi awa: Aliyense amenene akudziwa munthu amene ana- pha Layasi, mwana wa Ladaka, abwere kudzanditsina khutu. Ndipo ngati munthu amene anachita zimenezi akundimva, angobwera yekha mwawulemu zinthu zisanafike poyipa. Akabwera yekha ndimuchitira chifundo, koma akapanda kutero akhala akungodzikolezera moto. Mu- nthu amene angabwere yekha tingomuthamangitsa mumzinda uno ndi- po salandiranso chilango china kuwonjezera pamenepo. Komanso ngati wina akudziwa kuti amene anapha mfumuyi ndi munthu yemwe sa- khala mumzinda uno, asakhale chete. Ngati munthu wotero atabwera kwa ine n’kudzandinong’oneza, ndimupatsa chiwongoladzanja chochu- luka zedi. Koma akangoyerekeza kukhala chete, kapena ngati ame- ne anapha munthuyu atapanda kudziwulula, kapenanso ngati munthu amene akudziwa munthu yemwe anachita zimenezi atayerekeza kubisa mnzake, awona mikwingwirima. Mumvetseretu mosamala zimene ndikunenazi. Ndikunena kuti musayerekeze kubisa mnzanu. Mulungu 7