Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 11
Sewero la Mfumu Edipa
KIREYO: Onse anaphedwa, kupatulapo m’modzi. Munthuyo atafika
kuno anafotokoza zonse zimene anawona. Koma pali chimodzi chimene
sankafotokoza bwinobwino.
EDIPA: N’chiyani chimene sanafotokoze bwinobwinocho? Mwina
kudziwa zimenezo kungatithandize kuwona ulusi womwe tingatole
kuti titsate nkhaniyi. Tikapanda kuchidziwa tikhoza kumangopupulika
m’mabodza n’kupezeka kuti tayamba kuyenda tikufuka utsi.
KIREYO: Anatiwuza kuti mfumuyo inaphedwa ndi achifwamba, osati
munthu m’modzi, koma gulu la achifwamba. Ankati achifwambawo
anawawukira mwamphamvu kwambiri moti zinali zosatheka kupulu-
mutsa mfumuyo.
EDIPA: Ndikuganiza kuti pali munthu winawake ku Thebesi kuno
yemwe anawatuma kuti achite zamtopolazi.
KIREYO: Ifenso tinkaganiza choncho. Koma Layasi atangophedwa, tina-
kumananso ndi vuto lina lowopsa kwambiri lomwe linatiphimba m’ma-
so n’kutilepheretsa kubwezera anthu okhetsa mwaziwo.
EDIPA: Koma zowona zimenezo? Mukundiwuza kuti mfumu ya mzinda
uno kuphedwa inu n’kuyiwala kulanga anthu oyipa omwe anayipha?
Koma ndiye munalakwitsadi kwambiri! Ndi vuto lanji lomwe linafika
pokupanikizani mpaka kuyiwala kulanga anthu omwe anachita chosalu-
ngama chimenechi?
KIREYO: Chinali chilombo chowopsa chija, chija chinkayimba nyimbo
yosadziwika. Chilombocho n’chimene chinachititsa kuti tiyike nkhani
yofunikayi pambali. Tisanameyi, miyoyo yathu inali pachiswe.
EDIPA: Popeza zinachitika zinatha, ndiyesetsa kuchitanso zofanana ndi
zimene ndinachita pa nthawi imene ija. Koma dziwani kuti n’zomveka
kuti Apolo atilange chonchi chifukwa tinachita zinthu molekerera kwa-
mbiri. Choncho ndigwira ntchito limodzi ndi mulungu wathuyu koma-
nso inuyo, kuti tipeze anthu amene anapha mfumuyi. Ndikuyenera ku-
chotsa chodetsa chimenechi msanga chifukwa n’kutheka kuti anthu ame-
newo angakhale akulinganizanso zoti andisowetse ineyo. Choncho ngati
nditabwezera imfa ya Mfumu Layasi, ndiye kuti ndadzipulumutsanso
ndekha. Choncho nyamukani nonse mupite kukayitana anthu onse kuti
6