Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 10
Sewero la Mfumu Edipa
KIREYO: Chabwino, Apolo wanena kuti ngati tikufuna kuti miliriyi ithe,
tichotse chinthu chimene chikudetsa mzinda wathuwu. Akuti ngati tita-
panda kutero, tonse tikhala chipere.
EDIPA: Ndiye tichotsa bwanji chodetsacho?
KIREYO: Anati tichotse amene anakhetsa magazi a munthu wosalakwa.
Akuti tikufunika kuchitapo kanthu kuti tibwezere imfa yake. Tikango-
tero mavutowa athera pomwepo.
EDIPA: Ndiye mulunguyo anakuwuza mayina a anthu omwe anapha
munthuyo?
KIREYO: Popeza mwafunsa, ndikuwuzani. Inuyo musanabwere kuno,
n’kuyamba kuyendetsa chombo cha ufumuwu, amene ankatilamulira
anali Mfumu Layasi.
EDIPA: Ndinamvadi zimenezo, kungoti nkhani yake sindimayidziwa
bwinobwino.
KIREYO: Mfumu Layasi inaphedwa mopanda chilungamo. Ndiye pano-
pa mulungu wathu wanena mosapita m’mbali kuti anthu amene anapha
mfumuyi ayenera kulangidwa mosasamala kanthu kuti amachokera
m’banja lotani.
EDIPA: Anakuwuza kumene anthuwo amakhala? Ngati sanatero, akuga-
niza kuti ndidziwa bwanji anthu amene anapha munthu zaka zambiri
zapitazo? Akufuna ndingolota?
KIREYO: Mulungu wathu wanena kuti anthuwo ali ku Thebesi konku-
no. Ngati titachenjera, tikhoza kuwambwandira, koma tikapusa timbwi-
ta.
EDIPA: Kodi mfumuyo inaphedwera kuti? Inali kunyumba kwake, ku-
munda kapena koyenda?
KIREYO: Inali kudziko lakutali. Pamene inkachoka kuno inanena kuti
inkapita ku Defi. N’zomvetsa chisoni kuti inayamba ulendowu, koma
siyinawumalize.
EDIPA: Palibe munthu aliyense amene anapulumuka n’kubwera kudza-
nena zimene zinachitika? Mwinatu titapeza munthu ameneyo akhoza
kutipatsa poyambira.
5