Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 9
Sewero la Mfumu Edipa
ndikunena pano, ndatumiza kale mlamu wanga, Kireyo, kuti akafunsire
kukachisi wa Pitiya Apolo ku Defi. Tikufuna akamufunse kuti tapalamu-
la chiyani kuti tikumane ndi tsokali. Tikufunanso tidziwe kuti akufuna
tichite chiyani kuti tiwonjole mzinda wathuwu pamoto. Koma ndikawe-
rengera masiku amene adutsa chichokereni Kireyo, nkhawa yayamba
kundigwira. Sindikudziwa kuti n’chiyani chikuchititsa kuti miyendo
yake imulemere n’kufika mpaka lero asanatulukire. Koma akangobwera,
ndikhale wotembereredwa ngati nditachita zosiyana ndi zimene mulu-
ngu wathu walamula. Ndichita chilichonse chimene akufuna kuti nonse
mupeze mpumulo.
WANSEMBE: Zimene mukunenazo ndi zowona, chifukwa wina wango-
nditsina khutu kuti Kireyo akubwera.
EDIPA: Mulungu wathu Apolo, tikomereni mtima kuti Kireyo abwere
ndi uthenga wabwino komanso wopatsa chiyembekezo.
WANSEMBE: Zikuwoneka kuti uthenga umene wabweretsa ndi wabwi-
no. Zikanakhala kuti watenga uthenga woyipa si bwenzi nkhope yake
ikuwala choncho, komanso si bwenzi atavala nkhata yamaluwa m’khosi
mwake. 4
4. Munthu amene wapita kukachisi wa Apolo n’kubwerako atavala nkhata yamaluwa m’khosi mwake ankhala kuti
watenga uthenga wabwino.
EDIPA: Boladi zitero. Tiyeni tingodikira atiwuze zimene mulunguyo
wanena. [Ak ulo wa KIREYO. EDIPA ak um uyitana atango tuluk ira.]
M’bale wanga Kireyo, Apolo wakuwuza zotani?
KIREYO: Wandiwuza uthenga wabwino ndipo ndikukhulupirira kuti
ngati titatsatira malangizo amene wapereka, mavutowa atichoka.
EDIPA: Chonde usamayankhule mozungulira. Ingotumbula, ungatiko-
mole ndi nkhawa.
KIREYO: Bwanji ndikakuwuzireni poduka mphepo? Komabe ngatinso
mukufuna, ndikhoza kukuwuzirani pompano anthuwa akumva. Izo zili
ndi inu.
EDIPA: Yakhula aliyense akumva. Anthu amenewa akufunika adzimvere
okha mumtolo. Ululu umene ndikumva chifukwa cha anthu amenewa
ndi wawukulu kuposa umene mayi amamva pobereka.
4