Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Sewero la Mfumu Edipa | Page 32
Sewero la Mfumu Edipa
nopompano.
YOKASI: Mkazi wanga, ndikuchita mantha kuti ndayankhula kale za-
mbiri. N’chifukwa chake ndikufuna kuti munthu ameneyo abwere mwa-
msanga.
YOKASI: Chabwino abwera posachedwapa. Koma tsopano mbuyanga,
chonde ndiwuzeni chimene chikukudetsani nkhawa chonchi.
EDIPA: Nkhawa yomwe ndili nayo yandikulira moti sindikubisiranso
chilichonse. Kwa ineyo palibenso wina yemwe ndingamuwuze zaku-
khosi kwanga kuposa iweyo. Bambo anga ndi a Polebasi a ku Korinto,
pomwe mayi anga ndi a Marope a ku Doriya. Chifukwa cha mphamvu
zimene ndinali nazo kwathu, anthu ankandilemekeza kwambiri kufikira
pamene mnzanga wina woledzera anayamba kundinena kuti ndine
mwana wopanda bambo komanso mayi. Ankati a Polebasi si bambo
anga enieni. Ndisanameyi, nkhani imeneyi inandisokoneza maganizo
kwambiri. N’zowona kuti sindinamuyankhe, koma ndinachita zimenezo
modziletsa kwambiri. Tsiku lotsatira ndinapita kwa makolo anga n’ku-
kawafotokozera nkhaniyo. Atamva zimene zinachitikazo, nawonso ana-
kwiya kwambiri. Iwo ananditsimikizira kuti ndine mwana wawo. Koma-
be, kamtima kena kankandiwuzabe kuti ndipitirize kufufuza nkhaniyo.
Chomwe chinkandiwawa n’choti mbiri ya nkhaniyo inali itawanda mu-
mzinda wonse. Choncho ndinaganiza zopita ku Defi mwachinsinsi kuti
ndikafufuze zowona zake. Koma sindinawuze mayi komanso bambo
anga. Nditafika ku Defi, Apolo sananene chilichonse chomveka. Anka-
ngondiwuza zinthu zodabwitsa zokhazokha. Ankati ndidzachita zinthu
zochititsa manyazi kwambiri komanso ndidzakumana ndi mavuto osa-
neneka. Ananenanso kuti ndidzapha bambo anga n’kukwatira mayi
anga, kenako n’kubereka nawo ana. Nditamva zimenezi, ndinatsimikiza
mtima kuti sindidzabwereranso ku Korinto. Kungochokera tsiku lime-
nelo, ndinasiyiratu kukutenga ngati kwathu. Posafuna kuti ulosiwu
ukwaniritsidwe pa ine, ndinayamba kukhala moyo woyendayenda. Pa-
mene ndinkathawa themberero limenelo, ndinadutsa pamalo ena omwe
panakumana misewu itatu. Pamenepo ndinakumana ndi anthu akuye-
nda pambali pagaleta lokokedwa ndi mahatchi. M’galetalo munali mu-
nthu wachikulire, yemwe anali ndi mawonekedwe ofanana ndi amene
27