Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 8

Paphata pa Chichewa Amagazi: Amphamvu. Chitsanzo: Ndife anyamata amagazi. Amakanyanga nsambo: Waluso kwambiri poimba gitala. Chitsanzo: Nthawi imeneyo amene ankakanyanga nsambo anali achina Michael Yekha, Tambala Chitenje ndi ena otero. Amalinyero: Anthu opalasa ngalawa, ogwira ntchito muboti. Chitsanzo: Kuoloka nyanja zikuluzikulu kumafuna amalinyero odziwa bwino ntchito. Amandikhumba: Amafuna kuputana nane, amandiyamba. Chichewa chimenechi chinkakonda kuyankhulidwa ndi ana akayambana. Akazindikira kuti wina amamukhumba, ankatenga dothi n’kumuuza kuti aphume. Akaphuma ankayamba kumenyana. Tanthauzo lake lenileni ndi kukufuna. Chitsanzo: Mwana ameneyu amandikhumba. Amandiyang’ana ndi diso la nkhwezule: Amaoneka kuti amadana nane, sandiona bwino. Chitsanzo: Bambo amenewa amandiyang’ana ndi diso la nkhwezule. Amashiwi: Malo okhala mbalame yopatsa mwayi. Angatanthauze munthu amene ukuganiza kuti angakuthandize kupeza zimene ukufuna. Chitsanzo: Wawaona amashiwi! Amasunga mawu ake: Amakwaniritsa zimene wanena. Chitsanzo: Mfumuyi imasunga mawu ake. 7